Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Mlongo Lyudmila Ponomarenko

APRIL 15, 2021
RUSSIA

Mlongo Lyudmila Ponomarenko Wazaka 70 Akupirirabe Pomwe Akuzengedwa Mlandu

Mlongo Lyudmila Ponomarenko Wazaka 70 Akupirirabe Pomwe Akuzengedwa Mlandu

Tsiku Lopereka Chigamulo

Khoti la m’Boma la Leninskiy ku Rostov-on-Don, posachedwapa lipereka chigamulo pa mlandu wa Mlongo Lyudmila Ponomarenko. *

Zokhudza Mlongoyu

Lyudmila Ponomarenko

  • Chaka chobadwa: 1950 (ku Ola, M’dera la Magadan)

  • Mbiri Yake: Ankagwira ntchito yokonza magetsi koma panopa anapuma pantchito. Ali ndi ana awiri aakazi komanso zidzukulu ziwiri. Amakonda kuwerenga komanso kuluka. Ndipo Akusamalira mwamuna wake yemwe akudwala matenda aakulu.

  • Iye anasangalala kwambiri atadziwa dzina la Mlengi. Zinamufikanso pamtima atadziwa za cholinga cha Mulungu chokhudza dziko lapansi komanso anthu. Mu1998 anabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova

Mlandu Wake

Pa 6 June 2019, akuluakulu a boma anatsegulira Mlongo Lyudmila Ponomarenko mlandu. Ina mwa milandu yomwe akuzengedwa ndi monga kupereka malo ochitira misonkhano ya chipembedzo chomwe amati ndi gulu “loopsa” komanso kulalikira uthenga wa m’Baibulo kwa anthu ena.

Lyudmila ankayembekezera kuti nayenso adzazunzidwa ngati mmene zilili ndi abale ndi alongo ena ku Russia. Iye anafotokoza kuti: “Pa nthawi imene abale ndi alongo a ku Moscow komanso a m’dera la Taganrog anayamba kuzunzidwa, ndinadziwiratu kuti pangatalike bwanji aliyense wa ife ayambanso kuzunzidwa.”

Chifukwa cha ziletso zobwera ndi mliri wa COVID-19, a Mboni za Yehova sangathe kupita kukhoti kuti akalimbikitse abale awo pa nthawiyi ya mlanduwu. Pa mfundo imeneyi, mlongo Lyudmila anati: “Ndinkada nkhawa komanso ndinkadandaula ndikaganizira kuti ndikakhala ndekhandekha kukhoti. Choncho ndikamapita kukhotiko ndinkakonda kuimba nyimbo za Ufumu chapansipansi komanso kupemphera kwa Yehova. Zimenezi zinkandipatsa mphamvu. Mlanduwu ukamazengedwa sindinkachita mantha ndipo nthawi inkatha mofulumira kwambiri.”

Mlongo Lyudmila anafotokozanso mmene zimenezi zinakhudzira mwamuna wake komanso ana ake awiri, omwe si a mboni za Yehova. Iye anati: “N’zovuta kwambiri kwa [iwo] kumvetsa chifukwa chake ndikuimbidwa mlandu. Iwo akuda nkhawa kwambiri chifukwa akuona kuti thanzi langa likuipiraipira. Kwa nthawi yaitali, anthu a m’banja langa akhala akuona mavuto [amene ndikukumana] nawowa ndipo ndimakwanitsa kupirira chifukwa cha thandizo lawo.

Ngakhale kuti mlongoyu akuzunzidwa amachitabe khama. Iye anati: “Ndili ndi chimwemwe chodzadza tsaya, chifukwa sindikuyenera kuopa chilichonse pa zimene zikundichitira panopa ngakhalenso zimene Baibulo limalosera kuti zichitika posachedwapa. Ubwenzi wanga ndi Yehova walimba kwambiri ndipo mapemphero anga amakhala ochokera mumtima, aatali komanso apadera kwambiri.”

Tikudziwa kuti Mlongo Ponomarenko apitiriza kulandira mzimu wa Yehova komanso madalitso amene amabwera chifukwa chokhala “mumthunzi wa Wamphamvuyonse.”—Salimo 91:1.

^ Nthawi zina n’zovuta kudziwiratu tsiku lenileni limene khoti lidzapereke chigamulo.