Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Mlongo Olga Ganusha

23 JUNE 2021
RUSSIA

Mlongo Olga Ganusha Amadalira Pemphero Kuti Apirire Pozunzidwa

Mlongo Olga Ganusha Amadalira Pemphero Kuti Apirire Pozunzidwa

UPDATE | Khoti la ku Russia Lagamula Kuti Mlongo Olga Ganusha Asapite Kundende Koma Azitsatira Malamulo Ena Ali Kunyumba

Pa 13 July 2021, khoti la m’boma la Voroshilovskiy ku Rostov-on-Don linapereka chigamulo chae pa mlandu wa Mlongo Olga Ganusha. Chigamulo chake ndi chakuti azitsatira malamulo ena ali kunyumba kwawo ndipo asapite kundende

Tsiku Lopereka Chigamulo

Posachedwapa, khoti la m’boma la Voroshilovskiy ku Rostov-on-Don lipereka chigamulo chake pa mlandu wa Mlongo Olga Ganusha. a Woimira boma pa mlanduwu sanatchule chilango chimene akufuna kuti mlongoyu apatsidwe.

Zokhudza Mlongoyu

Olga Ganusha

  • Kubadwa: 1961 (Ku Rostov-on-Don, m’chigawo cha Rostov)

  • Mbiri yake: Mlongoyu anapuma pa ntchito ndipo ali ndi mwana mmodzi wamwamuna. Amakonda kupanga zinthu zosiyanasiyana pamanja, kumvetsera nyimbo komanso kuwerenga mabuku.

  • Anayamba kuphunzira Baibulo atamva kuti pali chiyembekezo chodzakhala m’dziko lamtendere limodzi ndi abale athu komanso anzathu amene anamwalira. Mu 1995, anabatizidwa kukhala wa Mboni za Yehova.

Mlandu Wake

Chakumayambiriro kwa chaka cha 2019, apolisi ku Russia anazemba n’kukaika zipangizo zojambulira mawu ndi mavidiyo kunyumba imene Mlongo Olga Ganusha. Iwo anagwiritsa ntchito zimene anajambulazo ngati umboni wowalola kukapanga chipikisheni m’nyumbayo mu June 2019. Anafufuzanso zimene mlongoyu ankalemba, makalata ndi timabuku. Kenako anatsegulira Olga mlandu pa 17 August, 2020, womwe unayamba kuzengedwa pa 4 March, 2021. Milandu imene akuzengedwa ndi yoti amalola kuti kwawo kuzichitika misonkhano ya gulu loletsedwa komanso kuuza anthu ena zimene amakhulupirira. Mlongo Lyudmila Ponomarenko ndi Mlongo Galina Parkova ankafufuzidwanso pa mlandu womwewu koma panopa akuimbidwa mlandu wina.

Pa zaka ziwiri zimene Olga wakhala akufunsidwa mafunso komanso kuimbidwa mlandu wakhala akupeza mphamvu chifukwa chotchula zinthu mwachindunji m’mapemphero ake opembedzera. Olga anati: “Tsiku lililonse ndimapemphera kuti dzina la Mulungu liyeretsedwe kuposa m’mbuyo monsemu. Ndimapemphereranso abale ndi alongo amene atsekeredwa komanso amene ali pa ukaidi wosachoka panyumba kuti azipeza mphamvu komanso azitha kulalikira. Ndimawapempherera kuti azikhulupirira kwambiri Yehova ndipo asamakayikire kuti sadzatisiya pa nthawi ya mavuto.” Akaganizira zimene zikuchitika pa moyo wake amanena kuti: “Ndimapempha Yehova kuti andithandize kuti ndisamachite mantha koma ndizimudalira. Andithandize kukhala ngati chipilala chachitsulo kapena mpanda wamkuwa ngati mmene anachitira ndi Yeremiya. Ndikufuna ndithe kupirira mavuto okhala ngati moto ngati mmene anachitira Aheberi atatu aja. Ndikufunanso kuti ndizichita zinthu mwaulemu ngati mmene Yesu ankachitira ndi adani ake.”

Sitikukayikira kuti Yehova apitiriza kugwiritsa ntchito ‘dzanja lake lamanja lachilungamo’ pothandiza Olga ndi anzathu ena amene akuzunzidwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo.​—Yesaya 41:10.

a Nthawi zina sizitheka kudziwiratu tsiku lenileni lopereka chigamulo.