Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Mlongo Sona Olopova

30 JANUARY 2024
RUSSIA

Mlongo Sona Olopova Wagamulidwa Kuti Akagwire Ukaidi kwa Zaka Ziwiri

Mlongo Sona Olopova Wagamulidwa Kuti Akagwire Ukaidi kwa Zaka Ziwiri

Pa 25 January 2024, khoti la m’boma la Tsentralniy ku Tolyatti m’chigawo cha Samara, linagamula kuti Mlongo Sona Olopova ndi wolakwa ndipo anauzidwa kuti akagwire ukaidi kwa zaka ziwiri kundende ina. Mlongoyu akufunika kukhala m’ndende komanso kugwira ntchito zothandiza m’dera lake.

Zokhudza Mlongoyu

Tikukhulupirira kuti Yehova apitiriza kutsogolera, kuteteza komanso kukonda atumiki ake onse okhulupirika omwe sakusiya kumukhulupirira.​—Salimo 86:2.

Nthawi ndi Zochitika

  1. 15 May 2023

    Anamutsegulira mlandu

  2. 16 May 2023

    Apolisi anakafufuza m’nyumba yake. Anamufunsa mafunso komanso analetsedwa kupita madera ena.

  3. 6 September 2023

    Khoti linayamba kuzenga mlandu wake

  4. 25 January 2024

    Khoti linagamula kuti ndi wolakwa ndipo linalamula kuti akagwire ukaidi kundende kwa zaka ziwiri

a Mlongo Olopova analankhula zimenezi khoti lisanagamule mlandu wake.