Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Mlongo Svetlana Monis ndi mwamuna wake Alam Aliyev

3 FEBRUARY 2021
RUSSIA

Mlongo Svetlana Monis Sakutekeseka Ngakhale Kuti Khoti Likhoza Kugamula Kuti Ndi Wolakwa

Mlongo Svetlana Monis Sakutekeseka Ngakhale Kuti Khoti Likhoza Kugamula Kuti Ndi Wolakwa

Tsiku Lopereka Chigamulo

Pa 4 February 2021, * khoti la m’boma la Birobidzhan lomwe lili m’dera loima palokha la Ayuda ku Russia, lidzalengeza chigamulo chake pa mlandu wokhudza Mlongo Svetlana Monis. Woimira boma pa mlanduwu sananene chilango chomwe akufuna kuti mlongoyu apatsidwe.

Zokhudza Mlongoyu

Svetlana Monis

  • Chaka chobadwa: 1977 (ku Lesozavodsk)

  • Mbiri yake: Ali ndi vuto la maso. Amakonda kuphunzira zinenero zina. Anaphunzira Chitchainizi, Chingerezi ndi Chijeremani. Analera mwana wake wamwamuna payekha kwa nthawi yaitali. Anatsegula resitilanti ya zakudya za Chitchainizi kuti azithandiza banja lake

    Ankavutika maganizo ndi zinthu zopanda chilungamo zomwe zikuchitika m’dzikoli, choncho anayamba kuphunzira Baibulo. Anabatizidwa mu 2005. Mu 2015 anakwatirana ndi Alam Aliyev yemwenso akuimbidwa mlandu wina

Mlandu Wake

Pa 26 September 2019, mkulu wa gulu la apolisi oona zachitetezo (FSB), dzina lake D. Yankin anasumira mlandu Mlongo Svetlana Monis. Khoti linanena kuti mlongoyu asamagwiritse ntchito galimoto yake kwa miyezi pafupifupi iwiri, ngakhale kuti amafunikira galimotoyi kuti azithandiza agogo ake azaka 91.

Kafukufuku wa nkhani ya mlongoyu anamalizidwa mu December 2019. Kenako akuluakulu a boma anapititsa mlanduwu kukhoti la m’boma la Birobidzhan.

Poganizira zimene zinachitika, Mlongo Svetlana anati: “Apolisi atabwera kunyumba kwathu kudzachita chipikisheni ndinachita zinthu modekha. Ndi pa nthawi imeneyi pamene koyamba pa moyo wanga ndinamvetsa mawu akuti: ‘Odala ndi anthu amene akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo.’”—Mateyu 5:10.

Pambuyo pa zimenezi, mwamuna wa Mlongo Svetlana anatsekeredwa m’ndende kwa masiku 8. Iye anati: “Ndinkavutika kwambiri maganizo chifukwa sindinkadziwa kuti mwamuna wanga zikamuthera bwanji. Ndinkada nkhawa chifukwa ankavutika kwambiri ndi msana ndipo mlungu wapitawo anapita kuchipatala kukalandira thandizo . . . apolisi asanabwere kudzachita chipikisheni kunyumba kwathu. Zinali zosatheka kulankhulana naye moti sindinkadziwa ngati ali bwino kapena ayi. Ndinapemphera kwa Yehova n’kumuuza kuti ndikumukhuthulira nkhawa zanga zonse chifukwa ndikukhulupirira kuti amusamalira bwino kwambiri mwamuna wanga.”

Mlongo Svetlana sankakaikira kuti Yehova ali naye. Iye anati: “Pa nthawi yonseyi ndinaona Yehova akundithandiza. Ndinkaona kuti imeneyi si nthawi yolola kuti mavutowa andisokoneze. . . . Ndinayesetsa kuti ndisamangoganizira za ineyo. M’malomwake ndinkaganizira zomwe ndingachite kuti ndikhalebe wokhulupirika kwa Yehova.”

Kuti apitirizebe kuona zinthu moyenera, Mlongo Svetlana ndi mwamuna wake akuyesetsa kuchita zinthu zomwe zingawathandize kulimbitsa chikhulupiriro chawo. Mlongoyu anati: “Tsiku lililonse ine ndi mwamuna wanga timachitira limodzi lemba la tsiku komanso kuwerenga chaputala chimodzi cha m’Baibulo. Nthawi zonse timaganizira kwambiri Malemba amene angatitonthoze ndiponso kutilimbikitsa kuti tizidalira kwambiri Yehova.” Lemba la chaka cha 2019 limawatsimikizira a Svetlana ndi amuna awo kuti Yehova amawakonda. Lembali linali lochokera pa Yesaya 41:10 ndipo limati: “Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako.” Mlongoyu anati: “Tinapulinta vesili n’kulimata pakhoma.”

Kupirira kwa Mlongo kwathandiza kuti achibale awo omwe si Mboni ayambe kuona moyenera zimene a Mboni amakhulupirira. Mlongo Svetlana anati: “Panopa ndimakambirana mfundo za m’Baibulo ndi mayi anga omwe m’mbuyomu ankanditsutsa. Panopa amalemekeza kwambiri zomwe timakhulupirira ndipo nthawi zonse amandipepesa chifukwa cha zimene zikundichitikirazi. Agogo anga azaka 91 omwe ndi a chipembedzo cha Orthodox nawonso amatidera nkhawa chifukwa cha zimene zikutichitikira. Panopa anayamba kumvetsera mwachidwi tikamawafotokozera zimene Baibulo limaphunzitsa.”

Tikupitiriza kuganizira Mlongo Svetlana ndi mwamuna wake Alam. Tikudziwa kuti Yehova apitiriza kuwathandiza kukhala olimba mtima zomwe zidzawathandiza kuti asasiye kuona zinthu moyenera.—Salimo 10:17.

^ Tsikuli likhoza kusintha.