Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Mlongo Tatyana Obizhestvit

6 MAY, 2022
RUSSIA

Mlongo Tatyana Obizhestvit Amadalira Yehova

Mlongo Tatyana Obizhestvit Amadalira Yehova

Posachedwa Khoti la Mzinda wa Kazan lomwe lili m’Boma la Vakhitovskiy m’Chigawo cha Tatarstan lipereka chigamulo chake pa mlandu wa Mlongo Tatyana Obizhestvit. Loya wa boma sananene chilango chomwe akufuna kuti chiperekedwe kwa mlongoyu.

Nthawi Komanso Zomwe Zinachitika

  1. 19 January, 2020

    Apolisi anakafufuza zinthu m’nyumba mwa Mlongo Obizhestvit komanso m’nyumba zosiyanasiyana za a Mboni za Yehova ku Kazan. Mlongo Obizhestvit anawafunsa mafunso kenako anawatumiza kundende ina yongoyembekezera.

  2. 21 January, 2020

    Anawatulutsa m’ndende ndi kuwalamula kuti akhale pa ukaidi wosachoka panyumba.

  3. 25 May, 2021

    Anawatsegulira mlandu

Zokhudza Mlongoyu

Tikuyamikira kwambiri a Obizhestvit chifukwa cha chitsanzo chawo chodalira kwambiri Yehova m’malo modalira nzeru zawo pamene akupirira mavuto amene akukumana nawo.—Miyambo 3:5.