Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Mlongo Tatyana Sholner

JUNE 21, 2021
RUSSIA

Mlongo Tatyana Sholner Akudalira Yehova Komanso Akusangalalabe Ngakhale Pamene Akuzunzidwa

Mlongo Tatyana Sholner Akudalira Yehova Komanso Akusangalalabe Ngakhale Pamene Akuzunzidwa

MMENE ZINTHU ZILILI PANOPA | Khoti la ku Russia Lagamula Kuti Mlongo Tatyana Sholner Azitsatira Malamulo Ena Ali Kunyumba

Pa 25 June 2021, Khoti la m’Boma la Birobidzhan lomwe lili m’dera loima palokha la Ayuda, linagamula kuti Mlongo Tatyana Sholner ndi wolakwa. Khotili linalamula kuti mlongoyu azitsatira malamulo ena ali kunyumba kwa miyezi 30. Sakufunika kukakhala kundende.

Tsiku Lopereka Chigamulo

Khoti la M’boma la Birobidzhan lomwe lili m’dera loima palokha la Ayuda, lipereka chigamulo chake posachedwapa pa mlandu wa Mlongo Tatyana Sholner. a Loya woimira boma pa mlanduwu wapempha khoti kuti ligamule kuti mlongoyu akakhale kundende kwa zaka 4.

Zokhudza Mlongoyu

Tatyana Sholner

  • Chaka chobadwa: 1993 (Birobidzhan)

  • Mbiri yake: Bambo ake anamwalira ali wamng’ono kwambiri, zomwe zinachititsa kuti iye ndi mchimwene wake aleredwe ndi mayi awo okha. Amagwira ntchito pa malo ena ogulitsira mankhwala. Amakonda masewera a ice skating, kukwera njinga, komanso kusewera mpira wa volleyball

    Anayamba kuphunzira Baibulo pamene ankaphunzira kusoka pa koleji ina yophunzitsa luso lamanja. Anachita chidwi ndi mnzake wa m’kalasi yemwe anali wa Mboni za Yehova. Chikhulupiriro chakuti akufa adzauka chinamutonthoza pamene msuweni wake wa zaka 12 anamwalira mu 2014. Anabatizidwa mu 2017

Mlandu Wake

Pa 6 February, 2020, akuluakulu a boma ku Russia mu mzinda wa Birobidzhan, anatsegulira mlandu alongo 6 kuphatikizapo mlongo Tatyana wa zaka 27. Mlongoyu pamodzi ndi alongo enawo, akuimbidwa mlandu ochita zinthu “zoopsa,” chabe chifukwa choti amachita zinthu zokhudzana ndi chipembedzo chawo. A Mboni za Yehova okhala m’dera loima palokha la Ayuda akuimbidwa milandu yokwana 19.

Tatyana akukhulupirira kuti Yehova akumuthandiza kuti apirire mavuto amene akukumana nawowa. Iye ananena kuti: “Pamene mlandu wanga unayambika, sindinkachitanso zinthu zokhudza kulambira ngati mmene ndinkachitira poyamba, koma kuwerenga Baibulo kokha ndiye sindinaiwale. Ndinkamuuza Yehova zonse zomwe zinali mumtima mwanga komanso zomwe zinkandidetsa nkhawa. Ndinapemphera kuti andipatse mzimu wake woyera kuti undithandize kupirira komanso kuti ndikhalebe wokhulupirika mpaka mapeto. Ndinapempheranso kuti andithandize kukhala wolimba mtima komanso andipatse nzeru kuti ndikakwanitse kuikira kumbuyo dzina lake m’khoti.”

Anapitirizanso kuti: “Kudziwa kuti Yehova amathandiza komanso kuteteza atumiki ake kunandithandiza kuti ndikhalabe wosangalala. Yehova wandigwira mwamphamvu ndi dzanja lake lamanja. Zimenezi zandithandiza kuti ndizimudalira kwambiri komanso kuti ndikhale odekha pamene ndikukumana ndi mayesero.”​—Yesaya 41:10.

Pamene tikudikira chigamulo cha khoti pa mlanduwu, tikukhulupirira kuti ndi thandizo la Yehova, Tatyana apitirizabe ‘kupirira chisautso.’​—Aroma 12:12.

a Tsiku lenileni lopereka chigamulo nthawi zina silimadziwikiratu.