Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Mlongo Lyudmila Shut

APRIL 30, 2021
RUSSIA

Mlongo Wolumala wa Zaka 73 Akudalira Yehova Pamene Akumuimba Mlandu

Mlongo Wolumala wa Zaka 73 Akudalira Yehova Pamene Akumuimba Mlandu

MMENE ZINTHU ZILILI PANOPA | Khoti la ku Russia Lagamula Kuti M’longo Lyudmila Shut wa Zaka 73 Azitsatira Malamulo Ena Ali Kunyumba

Lolemba, pa 19 May 2021, Khoti la M’Boma la Nadezhdinskiy m’Chigawo cha Primorye, linagamula mlandu wa Mlongo Lyudmila Shut wa zaka 73. Mlongoyu anauzidwa kuti kwa zaka 4, azitsatira malamulo ena ali kunyumba kwake. Panopa mlongoyu sakuyenera kupita kundende.

Tsiku Lopereka Chigamulo

Khoti la M’Boma la Nadezhdinskiy m’Chigawo cha Primorye, posachedwapa lilengeza chigamulo cha mlandu wa Mlongo Lyudmila Shut. * Loya woimira boma pa mlanduwu akufuna kuti kwa zaka 4 mlongoyu azitsatira malamulo ena ali kunyumba kwake.

Zokhudza Mlongoyu

Lyudmila Shut

  • Chaka chobadwa: 1947 (Ku Chilumba cha Makarov Sakhalin)

  • Mbiri yake: Anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova kumayambiriro kwa chaka cha 2000. Ankasangalala kwambiri ndi maulosi a m’Baibulo. Anabatizidwa mu 2003. Mwamuna wake anamwalira m’chaka chomwechi cha 2003. Ali ndi ana atatu ndi zidzukulu zitatu. Mlongoyu amalemphera kuyenda chifukwa cha matenda ndipo kuti ayende amachita kudalira anthu ena.

Mlandu Wake

Mu November 2017, aboma anayamba kulondalonda Mboni za Yehova m’mudzi wa Razdolnoye. Ndiyeno mu February 2020, iwo anatsegulira mlandu Mlongo Lyudmila Shut. Ngakhale kuti ndiwachikulire komanso amadwaladwala, iwo anamupatsa chilango choti asamachoke panyumba.

Zimene abomawa akhala akumuchita zapangitsa kuti matenda ake afike poipa kwambiri ndipo nthawi zina amavutika maganizo ndiponso kukhala wokhumudwa. Vuto lake la maso panopa lafika poipa kwambiri moti akufunikira opaleshoni komanso wapezeka ndi matenda osowa tulo. Mlongo Lyudmila akuona kuti Yehova akumuthandiza chifukwa chakuti akumudalira ndiponso kumukhulupirira kwambiri. Yehova akuthandiza mlongoyu pomupatsa “mtendere wosatha” mogwirizana ndi zimene analonjeza pa Yesaya 26:3.

Abale ndi alongo amene amasonkhana ndi Mlongo Lyudmila akhala akumuthandiza mwachikondi. Iye ndi wosangalala kwambiri chifukwa akudziwa kuti abale akumupempherera. Mlongoyu anati: “Sindidzaiwala zimenezi.”

Mwana wake wamwamuna komanso wamkazi si a Mboni za Yehova koma akhala akumuthandiza kwambiri pa nthawi yovutayi.

Pamene akudikirira mlandu wake, tikupemphera ndi chikhulupiriro chonse kuti Mlongo Shut apitiriza kudalira “mphamvu ya Mulungu.”​—2 Timoteyo 1:8.

^ N’zovuta kudziwiratu tsiku lenileni limene khoti lidzapereke chigamulo.