Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Mlongo Yekaterina Pegasheva

8 APRIL, 2021
RUSSIA

Mlongo Yekaterina Pegasheva Ndi Wokhulupirikabe Pamene Akuyembekeza Chigamulo ku Russia

Mlongo Yekaterina Pegasheva Ndi Wokhulupirikabe Pamene Akuyembekeza Chigamulo ku Russia

MMENE ZINTHU ZILILI PANOPA | Khoti la ku Russia Lagamula Kuti Mlongo Yekaterina Pegasheva Azikatsatira Malamulo Ena Ali Kunyumba Kwawo

Pa 31 May, 2021, khoti la m’boma la Gornomariyskiy ku Republic of Mari El linapereka chigamulo chake kwa Mlongo Yekaterina Pegasheva. Iye anauzidwa kuti azikatsatira malamulo ena ali kunyumba kwawo kwa zaka 6 ndi hafu. Choncho panopa mlongoyu sapita kundende.

Tsiku la Mlandu

Posachedwapa a khoti la m’boma la Gornomariyskiy ku Republic of Mari El lipereka chigamulo pa mlandu wa mlongo Yekaterina Pegasheva.

Zokhudza Mlongoyu

Yekaterina Pegasheva

  • Kubadwa: 1989 (M’chigawo cha Gaintsy, Kirov)

  • Mbiri yake: M’banja lawo anabadwa yekha. Amakonda kuwerenga mabuku, kulemba ndakatulo komanso kuimba nyimbo. Amagwira ntchito yokonza m’nyumba. Anaphunzira chilankhulo cha Chimari kuti awonjezere utumiki wake

Mlandu Wake

Pa 3 October, 2019, Mlongo Pegasheva anamangidwa mumzinda wa Ain Yoshkar-Ola womwe ndi likulu la Republic of Mari El. Apolisi anachita chipikisheni m’nyumba yake ndipo analanda mabuku, zinthu monga mafoni, makalata komanso mapepala ena. Mlongoyu anamangidwa pa mlandu woti akuchita zinthu ndi gulu loletsedwa chifukwa choti ankakambirana nkhani za m’Baibulo ndi okhulupirira anzake.

Yekaterina anati: “Mwadzidzidzi apolisi anandigwira pamsewu n’kundikanikizira kumtengo manja anga ali kumbuyo. Ndinapemphera mwachidule ngati Nehemiya kuti Yehova andithandize.” Atamugwira anamutsekera kwa masiku oposa 100 podikira mlandu wake. Panopa ali pa ndende yosachoka pakhomo.

Yekaterina ankapanikizidwa ndi mafunso pa nthawi imene anatsekeredwayo. Iye ananona kuti zimene anaphunzira m’Baibulo zinamuthandiza. Iye anati: “Ndinkakumbukira zimene ndinaphunzira ku Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu. Mfundo imodzi imene inandilimbikitsa kwambiri inali yakuti: Ukamayankha anthu pamene akukufunsa umakhalanso utaima pamaso pa Ambuye Yesu. Izi zinandithandiza kuti ndikhale wodziletsa komanso ndizilemekeza anthu amene akundiimba mlandu mopanda chilungamo.”

Nthawi yomwe Mlongo Yekaterina anatsekeredwa komanso kuuzidwa kuti akhale pa ukaidi wosachoka pakhomo ikupitirira chaka chimodzi ndipo yakhala yovuta kwambiri. Iye wakhala akudwala ndipo sangathe kugwira ntchito iliyonse. Zimamupweteka kwambiri kuti amusiyanitsa ndi mayi ake komanso agogo ake. Ngakhale kuti wakumana ndi mavuto ambiri chonchi, Yekaterina watsimikiza kuti akhalabe wokhulupirika. Iye anati: “Pamene akundipanikiza kwambiri mpamene ndimavala kwambiri zida zochokera kwa Mulungu.” Iye ananenanso kuti: “Panopa sindikuopa chilichonse. Poyamba ndinali wolimba mtima koma pano mzimu wa Mulungu wandithandiza kuti ndikhale wolimba mtima kwambiri.”

Pamene Yekaterina akudikira chigamulo, sitikukayikira kuti apitiriza kudalira Yehova amene amapereka mphamvu kwa atumiki ake onse.—Ekisodo 15:2.

a Nthawi zina sizitheka kudziwiratu tsiku lenileni lopereka chiweruzo