Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Mlongo Barmakina ndi amuna ake a Dmitriy

SEPTEMBER 28, 2020
RUSSIA

Mlongo Yelena Barmakina Akhoza Kuikidwa M’ndende Chifukwa Chopemphera ndi Kuwerenga Baibulo

Mlongo Yelena Barmakina Akhoza Kuikidwa M’ndende Chifukwa Chopemphera ndi Kuwerenga Baibulo

Tsiku Lopereka Chigamulo

Pa 29 September 2020, * khoti la m’boma la Pervorechenskiy ku Vladivostok, lidzapereka chigamulo chake pa mlandu wokhudza Mlongo Yelena Barmakina. Mlongoyu akhoza kupatsidwa chigamulo chakuti azitsatira malamulo ena kunyumba kwake kwa zaka zitatu. Pamene Mlongo Barmakina akudikirira chigamulochi, khoti likupitiriza kuzenga mlandu amuna ake a Dmitriy.

Zokhudza Mlongoyu

Yelena Barmakina

  • Chaka chobadwa: 1967 (Ku Cherepanovo, M’chigawo cha Novosibirsk)

  • Mbiri yake: Amasamalira makolo ake okalamba ndi agogo ake. Amakonda kwambiri kujambula zithunzi ndipo imeneyi ndiyo ntchito imene akugwira. Amakondanso kusambira ndi kukwera mapiri

  • Atayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, anatsimikizira kuti maulosi amene anakwaniritsidwa amapereka umboni wakuti Mulungu ndi wamphamvu kwambiri. Chikhulupiriro chake chinakula ataona kuti Yehova akuyankha mapemphero ake. Iye anakwatirana ndi mwamuna wake Dmitriy mu 2003

Mlandu Wake

Pa 28 July 2018, 7 koloko m’mawa, gulu la apolisi onyamula zida litavala zophimba kumaso, linakathyola chitseko cha nyumba ya agogo aakazi a Mlongo Yelena Barmakina omwe ndi azaka 90, n’kulowa m’nyumbayo. Mlongo Barmakina ndi mwamuna wake Dmitriy ankakhala kunyumbako kuti azisamalira agogowo. Kenako apolisi anamanga M’bale Barmakin n’kukamutsekera poyembekezera kumuzenga mlandu. Apolisiwo anaopseza Mlongo Barmakina pomuuza kuti, “Kenako ndiwe!”

Patatha chaka chimodzi aboma anatseka maakaunti onse akubanki a Mlongo Barmakina. Pa 6 August 2019, loya wa boma anamutsegulira mlandu Mlongo Barmakina chifukwa chopemphera, kuwerenga Baibulo komanso kuonera nkhani za m’Baibulo. Loya wa mlongoyu anapempha khoti kuti liimitse mlanduwu chifukwa zinthu zimene amaimbidwa nazo mlandu ndi zimene wina aliyense wopembedza amachita. Komabe woweruzayu anagwirizana ndi zimene woimira boma pa mlanduwu ananena zoti zimene anachita Mlongo Barmakina, ndi “zinthu zoopsa” zomwe ndi zoletsedwa pa malamulo a ku Russia.

Mlongo Barmakina akuvutika kwambiri maganizo komanso akuzunzika chifukwa cha milandu imeneyi. Panthawi imene amuna ake anali m’ndende poyembekezera kuwazenga mlandu, mlongoyu sanaonane nawo kwa masiku 447. Komanso ndi zovuta kuti Mlongo Barmakina apeze ntchito chifukwa nthawi ina iliyonse akhoza kuitanidwa kuti akaonekere kukhoti kapena akafunsidwe mafunso.

Chifukwa cha zimene takhala tikuphunzira m’Baibulo, sitikudabwa kuti akuluakulu a boma ku Russia ‘akukankha kwambiri’ abale ndi alongo athu n’cholinga chofuna kuwasiyitsa kukhala okhulupirika. Komabe, timatonthozedwa podziwa kuti Yehova apitirizabe kukhala ‘malo awo obisalapo ndi mphamvu zawo.’—Salimo 118:13, 14.

^ ndime 3 Detili likhoza kusinthidwa