Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Mlongo Yelena Reyno-Chernyshova

28 JANUARY 2021
RUSSIA

Mlongo Yelena Reyno-Chernyshova Akuimbidwa Mlandu Chifukwa Cholambira Mulungu

Mlongo Yelena Reyno-Chernyshova Akuimbidwa Mlandu Chifukwa Cholambira Mulungu

Tsiku Lopereka Chigamulo

Pa 29 January 2021, * khoti la m’boma la Birobidzhan lomwe lili m’dera loima palokha la Ayuda ku Russia lidzapereka chigamulo chake pa mlandu wa Mlongo Yelena Reyno-Chernyshova. Woimira boma pa mlanduwu sananene chilango chimene akufuna kuti mlongoyu apatsidwe.

Zokhudza Mlongoyu

Yelena Reyno-Chernyshova

  • Chaka chobadwa: 1968 (ku Maloy, m’chigawo cha Irkutsk)

  • Mbiri yake: Anaphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova cha m’ma 1990. Zimenezi zinachititsa kuti asiye ntchito ya usilikali yomwe ankagwira komanso anayesetsa kuti akhale ndi banja labwino. Anabatizidwa mu 1998

  • Ngakhale kuti mwamuna wake si wa Mboni koma samuletsa kutumikira Yehova. Amakonda kusewera mpira wamiyendo ndi volebo

Mlandu Wake

Pa 29 September 2019, khoti la m’boma la Birobidzhan linatsegulira mlandu Mlongo Yelena Reyno-Chernyshova.

Apolisi a gulu lachitetezo la FSB anapita kunyumba kwa Mlongo Yelena moopseza kukachita chipikisheni. Mlongoyu akuthokoza Yehova pomuthandiza kukhala wodekha pa nthawi imeneyi. Iye akuti: “Ndinapemphera kwa Yehova mosalekeza kuti andithandize kuchita zinthu modekha ndiponso molimba mtima, kuti ndichite zinthu mwaulemu komanso ndisamukhumudwitse. Pochita chipikishenichi, apolisi anachita zinthu modekha komanso mwaulemu.”

Mlanduwu wachititsa kuti Mlongo Yelena ndi banja lake akumane ndi mavuto aakulu. Mu July 2020, mwamuna wake anadwala matenda amtima kachitatu. Mlongoyu wauzidwa kuti asatuluke m’dera la Birobidzhan ndipo anamutsekeranso ma akaunti ake onse a kubanki.

Mlongo Yelena amalimbikitsidwa kwambiri akamaganizira zitsanzo za atumiki a Yehova ena omwe anakwanitsa kupirira pamene ankazunzidwa. Iye akuti: “Ndimakonda kuwerenga nkhani za abale ndi alongo amene nyumba zawo zinachitidwa chipikisheni komanso amene anazunzidwa chifukwa chotumikira Yehova. Iwo anakumana ndi mavuto ambiri komanso anachitiridwa zinthu zambiri zankhanza koma anapirira zonsezi molimba mtima.” Mlongoyu amalimbikitsidwanso kwambiri chifukwa choti nthawi zonse amawerenga Baibulo ndi kusinkhasinkha.

Pamene akupitiriza kupirira, mlongoyu amakonda kuganizira mfundo za m’lemba la Yesaya 30:15, lomwe mbali yake ina imati: “Mudzakhala amphamvu mukakhala osatekeseka ndi achikhulupiriro.” Iye akufotokoza kuti: “Nthawi zonse ndimaganizira vesi limeneli. Ndikuthokoza kwambiri Yehova chifukwa choti anandikokera m’gulu lake . . . Nthawi zonse ndimakhala ndi mtendere wamumtima. Ndimadalira kwambiri [Yehova] panopa ndipo sindikayikira kuti azindithandiza pa chilichonse. Ndikudziwa kuti sadzandisiya ngakhale pang’ono.”

^ Detili likhoza kusinthidwa.