Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Msonkhano wa atolankhani ku Moscow pa 1 April 2021, wokumbukira kuti papita zaka 70 kuchokera pamene a Mboni za Yehova anasamutsidwa pa sitima kupita ku Siberia

5 APRIL, 2021
RUSSIA

Msonkhano wa Atolankhani ku Moscow Wokumbukira Zinthu Zankhanza Zimene Zinachitika Zaka 70 Zapitazo

A Mboni za Yehova Pafupifupi 10,000 Anawasamutsira ku Siberia

Msonkhano wa Atolankhani ku Moscow Wokumbukira Zinthu Zankhanza Zimene Zinachitika Zaka 70 Zapitazo

Pa 1 April 2021, ku Moscow kunali msonkhano wa atolankhani wokumbukira nkhanza zimene boma la Soviet Union linachitira a Mboni za Yehova zaka 70 zapitazo. Mu 1951, a Mboni za Yehova pafupifupi 10,000 anawanyamula pa sitima m’mayiko 6 a Soviet Union kupita nawo ku Siberia. Ntchito imeneyi ankaitchula kuti Operation North. Pamwambowu, panali anthu 6 amene analankhula komanso kuyankha mafunso ndipo ena mwa anthuwa anali akatswiri a zamaphunziro komanso a za ufulu wa anthu. Sikuti akatswiriwa anangokambirana za nkhanza zimene zinachitika pa nthawiyo, koma anazigwirizanitsanso ndi zimene boma la Russia likuchita panopa pozunza a Mboni. Anthu anaoneranso msonkhano wonsewu kudzera pa Intaneti.

M’bale Yaroslav Sivulsky, yemwe amaimira bungwe la Mboni za Yehova ku Europe analankhulanso pamwambowu. Achibale ake a m’bale Sivulsky analinso m’gulu la anthu amene anapititsidwa ku Siberia. Iye analankhula kwa nthawi yaitali za nkhanza zimene zinachitika posamutsa anthu. Iye ananena kuti: “Titachita kafukufuku tinapeza kuti a Mboni okwana 9,793 ndi mabanja awo anathamangitsidwa. Nambala imeneyi ikuphatikizapo anthu amene anafa komanso kubadwa paulendowu.”

Katswiri wina wa zachipembedzo ku Russia, dzina lake Sergey Ivanenko, anafotokoza zimene boma la Soviet Union linkachita pofalitsa nkhani zabodza zokhudza a Mboni za Yehova ndipo anazigwirizanitsa ndi zimene boma la Russia likuchita panopa pozunza a Mboni za Yehova. Ivanenko anatsindikanso mfundo yakuti a Mboni za Yehova ndi anthu opirira kwambiri. Iye ananena kuti, “Nkhanza zoopsa zimene boma la Russia lakhala likuchitira a Mboni za Yehova kuyambira mu 2017 ndi zosathandiza. Zimene a Mboni za Yehova anachita popirira nkhanza mu ulamuliro wa Soviet Union komanso zimene a akuchita panopa ku Russia, popitirizabe kuikira kumbuyo zimene amakhulupirira, ndi umboni wosonyeza kuti n’kungotaya nthawi kulimbana nawo. Apa chinthu chanzeru chimene boma la Russia lingachite ndi kuchotsa lamulo loletsa ntchito ya Mboni za Yehova.”

Katswiri wina wa zachipembedzo ku Kazakhstan, dzina lake Artur Artemyev, yemwenso analemba kabuku kofotokoza mbiri ya Mboni za Yehova ku Kazakhstan, kakuti Jehovah’s Witnesses in Kazakhstan: A Social-Historical and Religious Analysis (kokonzedwanso mu 2020), ananena kuti nkhanza zoopsa kwambiri zimene boma la Soviet Union linachita sizinathetse ntchito ya Mboni za Yehova kapena kuwafooketsa. M’malomwake, a Mboni za Yehova anawonjezereka kwambiri pa nthawi ya ulamuliro wa Soviet. Nayenso katswiri woona za ufulu wa anthu, dzina lake Valery Borschev, yemwenso ali m’gulu lina loona za ufulu wa anthu (Moscow Helsinki Group) anati: “Chimene akuluakulu a boma ayenera kudziwa n’chakuti, kuzunza a Mboni kumangowapatsa mphamvu basi.”

Valentin Gefter, yemwenso amagwira ntchito ndi mkulu woyang’anira za ufulu wa anthu ku Russia (Commissioner for Human Rights in Russia) anakamba nkhani yakuti “Mmene Anthu Omangidwa Chifukwa cha Chikhulupiriro Chawo Akuchulukira ku Russia.” A Mboni ku Russia akumangidwa chifukwa cha zimene amakhulupirira osati pa zifukwa za ndale. Iye anati: “A Mboni za Yehova salimbana ndi boma.” A Gefter ananenanso kuti zimene a Mboni amakhulupirira zimangowalimbikitsa kuti asamalowerere ndale. Ndiye zimenezi zimachititsa kuti maboma aziwazunza kapena kuwamanga popanda zifukwa.

Amene analankhula komaliza ndi Aleksandr Verkhovsky. Iye ali m’bungwe lina loona za ufulu wa anthu (Presidential Human Rights Council) komanso ndi mkulu wa bungwe lina loona za malamulo ndi zamilandu. (SOVA Center for Information and Analysis) Bungwe lachiwirili limaona komanso kulemba za milandu yonse imene likuona kuti boma linagwiritsa ntchito molakwika lamulo lokhudza anthu ochita zinthu zoopsa, kuphatikizapo milandu ya a Mboni za Yehova. Iye anafotokoza mwatsatanetsatane mmene dziko la Russia likuzunzira anthu. Iye anafunsa kuti: “Kodi nkhanza zimene akuchitira a Mbonizi zikhoza kutha? Funso limeneli ndi lofunika koma yankho lake silikudziwika.” Verkhovsky akuona kuti boma la Russia liyenera kusiya kuzunza a Mboni za Yehova. Iye anatchula mfundo zina zimene opanga malamulo ayenera kutsatira n’cholinga choti ateteze dziko kwa anthu ochitadi zoopsa enieni osati kuphwanya ufulu wa anthu okonda mtendere ngati a Mboni.

Atolankhani analoledwa kufunsa mafunso pa mfundo zimene zinafotokozedwazo.

Pa tsiku lomweli, msonkhano wina unachitika mumzinda wa Chisinau ku Moldova, unakonzedwa ndi akuluakulu a bungwe lina komanso a mayunivesite awiri. (Institute of History of the Academy of Sciences of Moldova, Alecu Russo State University of Balti, ndi Bogdan Petriceicu Hasdeu State University of Cahul) Msonkhano wina wa atolankhani udzachitika ku Ukraine pa 9 April.