Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Valeriy Rabota

29 MARCH 2024 | INAKONZEDWANSO PA: 10 JULY 2024
RUSSIA

NKHANI YOKHUDZA M’BALE YEMWE WAPEZEDWA WOLAKWA | “Sindikudandaula Kapena Kuchita Mantha”

NKHANI YOKHUDZA M’BALE YEMWE WAPEZEDWA WOLAKWA | “Sindikudandaula Kapena Kuchita Mantha”

Pa 10 July, 2024, Khoti la m’boma la Khabarovsk linapeza kuti M’bale Valeriy Rabota ndi wolakwa ndipo linagamula kuti kwa zaka 6, azitsatira malamulo enaake ali panyumba. M’baleyu sakufunika kupita kundende panopa.

Zokhudza M’baleyu

Timayamikira M’bale Rabota chifukwa cha chitsanzo chake pa nkhani ya chikhulupiriro komanso tikudziwa kuti Yehova akhala naye ndipo akhalanso ndi onse amene apitirize kukhala okhulupirika.​—Salimo 37:28.

Nthawi Komanso Zimene Zinachitika

  1. 1 March 2022

    Anamutsegulira mlandu

  2. 3 March 2022

    Akuluakulu a boma anafufuza m’nyumba yake. M’baleyu anafunsidwa mafunso ndipo anamumanga n’kumutsekera kaye poyembekezera kumuzenga mlandu

  3. 5 March 2022

    Anamusamutsira kundende yodikirira kuti mlandu uzengedwe

  4. 29 June 2022

    Anamutulutsa n’kumuika pa ukaidi wosachoka panyumba

  5. 7 October 2022

    Anamumasula pa ukaidi wosachoka panyumba n’kumuika pa ukaidi wosapita m’madera ena

  6. 11 May 2023

    Anayamba kumuzenga mlandu