2 AUGUST, 2022
RUSSIA
Ndikunyadira Kuti “Ndapanga Nawo Mbiri ya Gulu Lathu”
Pa 26 July 2022, Khoti la Mzinda wa Snezhinskiy m’Chigawo cha Chelyabinsk linapeza kuti M’bale Ilya Olenin ndi wolakwa. Loya woimira boma anapempha khotili kuti lipatse M’bale Olenin chilango chokakhala kundende zaka 6 ndi hafu. Koma m’malo mwake, khoti linagamula kuti m’baleyu alipire ndalama za ku United States zokwana madola 8,150.
Nthawi Komanso Zimene Zinachitika
17 April, 2017
Apolisi a FSB anasokoneza Mwambo wa Chikumbutso. Panthawiyi apolisiwa ananena kuti M’bale Olenin ali ndi mlandu “wogwira ntchito yaumishonale.” Komabe mlanduwo unatsekedwa
30 November, 2020
Apolisi anakafufuza zinthu kunyumba kwa M’bale Olenin
28 September, 2021
M’bale Olenin anamutsegulira mlandu
28 October, 2021
Apolisi anabweranso kachiwiri kudzafufuza zinthu m’nyumba mwake. Pa nthawiyi anatenganso M’bale Olenin kuti akamufunse mafunso komanso anamuletsa kuti asapange ulendo uliwonse wochoka m’deralo
23 May, 2022
Khoti linayamba kuzenga mlandu
Zokhudza M’baleyu
Tikusangalala kwambiri kuti M’bale Olenin komanso abale ndi alongo athu onse akuyesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi dzina lathu poyesetsa kuchitira umboni za Mulungu wathu wamkulu Yehova.—Yesaya 43:10.