6 JANUARY 2023
RUSSIA
“Ndikupitirizabe Kudalira Yehova”
Posachedwapa khoti la mumzinda wa Nevinnomyssk m’chigawo cha Stavropol lipereka chigamulo pa mlandu wokhudza M’bale Sergey Kuznetsov. Loya waboma sananenebe chilango chomwe akufuna kuti khoti lipereke kwa m’baleyu.
Zokhudza M’baleyu
Njira imene Yehova akusamalirira a Kuznetsov imalimbitsa chikhulupiriro chathu kuti Iye amaona ‘masautso athu onse’ komanso ‘adzatikweza m’mwamba ndi kutinyamula’ pamene tikukumana ndi mavuto.—Yesaya 63:9.
Nthawi Komanso Zimene Zinachitika
21 November 2018
Apolisi anakafufuza zinthu m’nyumba za a Mboni za Yehova kuphatikizapo nyumba ya a Kuznetsov
12 December 2019
Anamutsegulira mlandu
18 June 2020
Anamuika pamndandanda wa anthu ochita zinthu zoopsa
31 May 2022
Anamuletsa kuti asatuluke m’dera la kwawo
7 September 2022
Mlandu unayamba kuzengedwa