Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Apolisi ku Russia anyamula zida zoopsa komanso hamala yayikulu ndipo akupita kukathyola imodzi mwa nyumba 31 za a Mboni zomwe anathyola mu July 2019 mumzinda wa Nizhniy Novgorod

AUGUST 7, 2019
RUSSIA

Nyumba za a Mboni Zomwe Zathyoledwa ndi Apolisi ku Russia Zapitirira 600

Nyumba za a Mboni Zomwe Zathyoledwa ndi Apolisi ku Russia Zapitirira 600

Kwa miyezi 18 yapitayi, apolisi komanso a gulu loona za chitetezo m’dziko la Russia (Federal Security Service), athyola komanso kulowa m’nyumba 613 za abale ndi alongo athu. Kuyambira January 2019, apolisi athyola n’kulowa m’nyumba 332 ndipo chiwerengerochi chikuposa chiwerengero cha nyumba zonse zomwe zinathyoledwa m’chaka chonse cha 2018, zomwe zinalipo 281.

Chiwerengero cha nyumba za abale ndi alongo athu zomwe zathyoledwa chakwera kwambiri m’miyezi yaposachedwapa. Nyumba 71 zinathyoledwa mu June, ndipo mu July nyumba 68 ndi zomwe zinathyoledwa. Chiwerengerochi n’chokwera kwambiri tikachiyerekezera ndi cha mu 2018 pomwe nyumba pafupifupi 23 ndi zimene zinkathyoledwa mwezi uliwonse.

Apolisi ku Russia athyola ndipo akulowa m’nyumba mumzinda wa Nizhniy Novgorod

Pa nthawi yomwe akuthyola nyumba, gulu la apolisi ovala zobisa nkhope omwenso amanyamula zida zambiri, limafika mwadzidzidzi panyumbayo n’kulowa. Akalowa m’nyumbayo, nthawi zina apolisiwo amalozetsa mfuti kunkhope za a Mboni, kuphatikizapo ana ndi achikulire, ngati kuti a Mboniwo ndi zigawenga zoopsa. Choncho n’zosadabwitsa kuti akatswiri ambiri akugwirizana ndi zomwe Dr. Derek H. Davis ananena. Dr. Davis anali mkulu wa yunivesite ina yomwe imachita maphunziro okhudza mgwirizano wa pakati pa zipembedzo ndi boma. (Baylor University’s J.M. Dawson Institute of Church-State Studies) Iwo anati: “Boma la Russia ndi limene likuchita zinthu ‘zoopsa’ pozunza mwankhanza gulu la mtendere la Mboni za Yehova.”

N’zomvetsa chisoni kuti pamene chiwerengero cha nyumba za abale athu zomwe zathyoledwa chikukwera, nachonso chiwerengero cha amene akuganiziridwa kuti apalamula milandu chikukwera. Panopa pali abale ndi alongo 244 amene awapeza ndi milandu ku Russia komanso ku Crimea. Chiwerengerochi chakwera kuwirikiza maulendo oposa awiri kuyambira mu December 2018, pomwe panali milandu 110. Pa abale ndi alongo 244 omwe anawapeza ndi milandu, 39 ali m’ndende, 27 ali paukaidi wosachoka panyumba, ndipo oposa 100 analetsedwa kuchita zinthu zosiyanasiyana.

Ngakhale kuti apolisi ku Russia akupitiriza kulimbana ndi abale ndi alongo athu, ‘sitikupatutsidwa ndi masautso amenewa.’ M’malomwake, timalimbikitsidwa tikamva malipoti oti abale athu akupitiriza kukhala okhulupirika komanso kupirira. Choncho tikutamanda ndiponso kuyamikira Yehova chifukwa choyankha mapemphero athu ambiri omwe timapereka m’malo mwa abale athuwa, ndipo tili ndi chikhulupiriro chonse kuti apitiriza kuchita zimenezi.—1 Atesalonika 3:3, 7.