25 AUGUST 2023
RUSSIA
“Palibe Chimene Chimandithandiza Kukhala Wosangalala Kwambiri Kuposa Kukhala pa Ubwenzi Ndi Yehova”
Posachedwapa, khoti la mumzinda wa Goryacheklyuchevskoy m’chigawo cha Krasnodar lilengeza chigamulo chake pa mlandu wokhudza M’bale Pavel Sidorenko. Woimira boma pa mlanduwu akuyembekezeka kusankha chilango chimene akufuna kuti m’baleyu apatsidwe.
Zokhudza M’baleyu
Mofanana ndi Pavel, nafenso timasangalala kudziwa kuti tikamachita khama kukhalabe pa “njira ya moyo,” tidzakhala ndi chimwemwe chosatha.—Salimo 16:11.
Nthawi Komanso Zimene Zinachitika
26 January 2022
Anayamba kuimbidwa mlandu
28 January 2022
Apolisi anakachita chipikisheni kunyumba kwawo. Anafunsidwa mafunso komanso analetsedwa kupita m’madera ena
22 March 2023
Khoti linayamba kuzenga mlandu wawo