NOVEMBER 19, 2019
RUSSIA
Woweruza Wina ku Russia Wagamula Kuti M’bale Dmitriy Barmakin Atulutsidwe Atakhala M’ndende Masiku 447
Patadutsa masiku 447 akusungidwa m’ndende, pa 18 October, 2019, M’bale Dmitriy Barmakin anauzidwa kuti akakhale pa ukaidi wosachoka panyumba. Iye anakumananso ndi mkazi wake Elena yemwe wakhala naye m’banja zaka 13.
M’bale Barmakin anamangidwa pa 28 July, 2018, pa nthawi yomwe anapita kukacheza kunyumba kwa agogo ake azaka 90. Kenako apolisi ovala zobisa nkhope komanso onyamula mfuti anathyola m’nyumbamo. M’bale Barmakin anaimbidwa mlandu wotenga nawo mbali pamisonkhano yachipembedzo cha Mboni za Yehova. Khoti la m’boma la Pervorechenskiy mumzinda wa Vladivostok, linagamula kuti a Dmitriy Barmakin asungidwe m’ndende kwa miyezi iwiri. Pambuyo pake, khotili linawonjezera nthawi yoti akhale m’ndende kwa maulendo ena 8.
Pa nthawi yomvetsera mlanduwu, khotili linanena kuti zimene M’bale Barmakin ankachita polambira Mulungu mwamtendere, ndi “mlandu wotsutsana ndi mfundo za m’malamulo oyendetsera dziko komanso chitetezo cha dziko.” Zimenezi ndi zabodza chifukwa n’zosemphana ndi zomwe zinalembedwa momveka bwino m’Gawo 28 la m’Malamulo Oyendetsera Dziko la Russia. Gawoli limati anthu onse akhoza “kusankha okha kuti akhale m’chipembedzo, kuuza ena mfundo zachipembedzo kapena zina, komanso kuchita zinthu mogwirizana ndi mfundozo.”
Tikusangalala kuti a Stanislav Salnikov omwe ndi woweruza milandu wa khoti la m’boma la Pervorechenskiy mumzinda wa Vladivostok, anagamula kuti M’bale Barmakin atulutsidwe m’ndende ngakhale kuti mlandu wa m’baleyu ukufufuzidwabe.
Tikukhulupirira kuti Yehova apitiriza kupereka mphamvu komanso kulimbikitsa abale ndi alongo athu a ku Russia, makamaka omwe ali m’ndende komanso pa ukaidi wosachoka panyumba. Abale monga M’bale Barmakin akusonyeza zitsanzo zabwino kwa abale ndi alongo padziko lonse pa nkhani ya kulimba mtima ndiponso kukhulupirika.—Afilipi 1:13, 14.