Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Mzere wapamwamba (kuyambira kumanzere): M’bale Aleksey Dyadkin, Aleksey Goreliy, ndi M’bale Nikita Moiseyev

Mzere wam’munsi (kuyambira kumanja): M’bale Vladimir Popov, Yevgeniy Razumov, ndi M’bale Oleg Shidlovskiy

24 MARCH, 2022
RUSSIA

Yehova Akuthandiza Mabanja a Anthu 6 Omwe Ali M’ndende Podikira Kuzengedwa Kwa Mlandu Wawo

Yehova Akuthandiza Mabanja a Anthu 6 Omwe Ali M’ndende Podikira Kuzengedwa Kwa Mlandu Wawo

Posachedwa, Khoti la Rostov-on-Don lomwe lili m’Boma la Leninskiy lipereka chigamulo chake pa mlandu wa M’bale Aleksey Dyadkin, Aleksey Goreliy, Nikita Moiseyev, Vladimir Popov, Yevgeniy Razumov ndi M’bale Oleg Shidlovskiy. Loya woimira boma sananene chigamulo chomwe akufuna kuti abalewa apatsidwe.

Nthawi Komanso Zimene Zinachitika

  1. 8 August, 2020

    Apolisi a FSB anakafufuza zinthu m’nyumba 17 za Mboni za Yehova m’mizinda itatu ya m’Chigawo cha Rostov komanso mumzinda wa Kursk. M’bale Goreliy, Moiseyev, Razumov ndi M’bale Shidlovskiy, anamangidwa ndipo tsiku lotsatira anakawatsekera m’ndende podikira kuzengedwa kwa mlandu wawo. M’bale Popov anaikidwa pam’ndandanda wa anthu omwe boma likuwafuna kwambiri.

  2. 12 August, 2020

    Apolisi a FSB anamanga M’bale Popov ndipo pambuyo pa masiku awiri, anamupititsa kundende kuti azikayembekezera kuzengedwa kwa mlandu wake.

  3. 21 August, 2020

    M’bale Dyadkin atapita kupolisi kuti akayankhe mafunso, anatumizidwa kundende kuti azikayembekezera kuzengedwa mlandu

  4. 28 June, 2021

    Loya anapita kundende kukakumama ndi abalewa. Anamufotokozera mavuto omwe akukumana nawo komanso kuti m’maselo mukumakhala mozizira kwambiri mpaka kufika madigirii 40 moti m’makoma mukumakhala mungu ndipo akaidi akupatsirana COVID-19

  5. 21 July, 2021

    M’bale Popov anapezeka ndi vuto lolephera kupuma ndipo anapita naye pakachipatala ka ndende ina. Kenako anamutumiza kuchipatala chachikulu

  6. 30 September, 2021

    Pambuyo pokhala m’chipatala kwa miyezi iwiri, M’bale Popov anabwerera nayenso kundende

  7. 17 November, 2021

    Mlandu unayamba kuzengedwa ndipo abale onse 6, anapitirizabe kuwasunga kundende

Zokhudza Abalewa

Tikupitiriza kupemphera kwa Yehova kuti athandize abale athuwa limodzi ndi mabanja awo. Tili ndi chikhulupiriro kuti Yehova apitiriza kuwapatsa mphamvu komanso kuwathandiza kukhalabe ndi chikhulupiriro.—Aroma 15:30.

a b c d e f Sitinakwanitse kucheza ndi abale 6 onsewa chifukwa adakawasungabe m’ndende