Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

kuyambira pamwamba kumanzere, kulowera kumanja mozungulira: Mlongo Maya Karpushkina; M’bale Nikolay Polevodov; M’bale Vitaliy Zhuk ndi mkazi wake Tatyana; M’bale Stanislav Kim ndi Mlongo Svetlana Sedova

23 MARCH, 2022
RUSSIA

Yehova Anathandiza Abale ndi Alongo Okhulupirika Okwana 6

Yehova Anathandiza Abale ndi Alongo Okhulupirika Okwana 6

Posachedwa khoti la m’Boma la Industrialniy m’Chigawo cha Khabarovsk, lipereka chigamulo pa mlandu wa Mlongo Maya Karpushkina, M’bale Stanislav Kim, M’bale Nikolay Polevodov, Mlongo Svetlana Sedova, M’bale Vitaliy Zhuk ndi mkazi wake Tatyana. Loya waboma sananene kuti anthuwa apatsidwe chilango chotani.

Nthawi Komanso Zimene Zinachitika

  1. 10 November, 2018

    Apolisi anasokoneza pate yomwe anthu 55 ankachita. Onse omwe ankachita pateyo kuphatikizapo ana, anapanikizidwa ndi mafunso, kutenga zidindo za zala zawo komanso kuwajambula zithunzi

  2. 12 November, 2018

    M’bale Kim, M’bale Polevodoc ndi M’bale Zhuk anakawatsekera m’ndende poyembekezera kuwazenga mlandu. Mlongo Karpushkina ndi Mlongo Zhuk anawaletsa kuti asatuluke m’dera lomwe amakhala

  3. 14 January, 2019

    M’bale Polevodoc ndi M’bale Zhuk anawatulutsa m’ndende n’kuwaika pa ukaidi wosachoka pakhomo

  4. 29 January, 2019

    M’bale Kim anamutulutsa m’ndende n’kumuika pa ukaidi wosachoka pakhomo

  5. 18 July, 2019

    Mlandu anausamutsira ku khoti la m’Boma la Industrialniy m’Chigawo cha Khabarovsk

  6. 2 August, 2019

    M’bale Polevodoc anamasulidwa pa ukaidi wosachoka pakhomo

  7. 9 September, 2019

    Mlandu wina wokhudza M’bale Kim komanso M’bale Polevodoc, unakaperekedwa kukhoti la Khabarovsk m’Boma la Zheleznodorozhniy

  8. 5 November, 2019

    M’bale Polevodoc anamuletsa kutuluka m’dera lomwe ankakhala

  9. 18 January, 2020

    M’bale Kim ndi M’bale Zhuk, anawamasula pa ukaidi wosachoka pakhomo

  10. 4 February, 2020

    M’bale Kim ndi M’bale Polevodoc anawapeza kuti ndi olakwa pa mlandu wina ndipo aliyense anagamulidwa kuti kwa zaka ziwiri, azitsatira malamulo ena ali kunyumba kwawo. Pa nthawi yonseyi Khoti la Khabarovsk la m’Boma la Zheleznodorozhniy, liziwayang’anira monga anthu opalamula mlandu

  11. 3 August, 2020

    Mlandu womwe unali ku Khoti la m’Boma la Industrialniy anaubweza kwa loya woimira boma ndipo loyayu anachita apilo

  12. 29 September, 2020

    Khoti la m’Chigawo cha Khabarovsk linalandira apilo ya loya waboma. M’bale Kim ndi M’bale Polevodoc anakaonekera pamaso pa jaji. Jajiyo anafotokoza kuti Dziko la Russia, mogwirizana ndi mayiko ena onse, linasainira nawo mgwirizano wa mayiko womwe umaletsa kuphwanya ufulu wopembedza kwa nzika zake

  13. 12 October, 2020

    Khoti la m’Chigawo cha Khabarovsk linagwirizana ndi chigamulo chomwe khoti la m’Boma la Industrialniy linapereka ndipo linabweza mlandu kwa loya waboma

  14. 15 December, 2021

    Mlandu unabwereranso ku khoti la m’Boma la Industrialniy

Zokhudza abale ndi alongowa

Tikudziwa kuti Yehova apitiriza kuthandiza abale ndi alongo athuwa komanso ena ambiri omwe akupanga “mtambo wa mboni waukulu” wamasiku athu ano.—Aheberi 12:1.