Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Anatoliy Isakov ndi mkazi wake, Tatyana

1 JANUARY 2024
RUSSIA

‘Yehova Sanandisiyepo’

‘Yehova Sanandisiyepo’

Posachedwapa khoti la mumzinda wa Kurgan m’chigawo cha Kurgan, lipereka chigamulo chake pa mlandu wokhudza M’bale Anatoliy Isakov. Loya woimira boma pa mlanduwu, adzafotokozabe chilango chomwe akufuna kuti m’baleyu apatsidwe.

Zokhudza M’baleyu

Timayamikira a Isakov chifukwa chokhala chitsanzo chabwino pa nkhani yolimba mtima komanso posonyeza chikhulupiriro ngakhale kuti akukumana ndi mavuto ambiri. Ndipo ndife oyamikira kwambiri kudziwa kuti kaya tikumane ndi zotani pa moyo wathu, Yehova adzapitiriza kukhala ‘thanthwe la mitima yathu.’​—Salimo 73:26.

Nthawi ndi Zochitika

  1. 13 July 2021

    Anawatsegulira mlandu

  2. 14 July 2021

    Apolisi anakafufuza m’nyumba yawo. Anaikidwa m’ndende kwa kanthawi kochepa

  3. 15 July 2021

    Anawasamutsira kundende poyembekezera kuwazenga mlandu

  4. 21 July 2021

    Anachita apilo kudipatimenti yoona za umoyo ya m’chigawo cha Kurgan kuti awamasule n’cholinga choti azikalandira thandizo la matenda a khansa

  5. 28 August 2021

    Anatulutsidwa m’ndende poyembekezera kuzenga mlandu wawo, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe litalamula koma analetsedwa kupita m’madera ena

  6. 6 July 2023

    Mlandu unayamba kuzengedwa