Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kuchokera kumanzere kupita kumanja: Mlongo Lyubov Galitsyna, M’bale Garegin Khachaturyan ndiponso M’bale Gevorg Yeritsyan

8 APRIL 2024 | INAKONZEDWANSO PA: 1 JULY 2024
RUSSIA

ZOKHUDZA ABALE NDI ALONGO OMWE ANAMANGIDWA | Amaona Kuti Yehova Amawasamalira Pamene Ali M’ndende Yoyembekezera Kuti Mlandu Wawo Uzengedwe

ZOKHUDZA ABALE NDI ALONGO OMWE ANAMANGIDWA | Amaona Kuti Yehova Amawasamalira Pamene Ali M’ndende Yoyembekezera Kuti Mlandu Wawo Uzengedwe

Pa 26 June 2024, khoti lamumzinda wa Novocherkassk m’chigawo cha Rostov linapeza kuti Mlongo Lyubov Galitsyna, M’bale Garegin Khachaturyan ndiponso M’bale Gevorg Yeritsyan ndi olakwa. Mlongo Galitsyna anagamulidwa kuti akakhale kundende kwa zaka ziwiri ndi miyezi itatu, koma khoti linaona kuti anagwira kale ukaidi wake potengera kutalika kwa nthawi yomwe anakhala kundende yodikirira kuti azengedwe mlandu. Sakufunika kupita kundende panopa. M’bale Khachaturyan anagamulidwa kuti akakhale m’ndende kwa zaka 6 ndi miyezi 6, pomwe M’bale Yeritsyan anagamulidwa zaka 6 ndi miyezi iwiri. Abale onsewa apita kundende.

Zokhudza Mlongoyu

Sitikayikira kuti ngakhale kuti anthu otsutsa amafuna kutichitira zoipa, Yehova apitiriza kudalitsa atumiki ake okhulupirika komanso kuwathandiza kuti zinthu ziwayendere ‘bwino.’​—Genesis 50:20.

Nthawi Komanso Zimene Zinachitika

  1. 11 August 2022

    Anatsegulira mlandu Lyubov, Garegin, ndi Gevorg. Nyumba zawo zinafufuzidwa. Garegin ndi Gevorg anaikidwa kundende ina yongoyembekezera

  2. 12 August 2022

    Garegin ndi Gevorg anasamutsidwira kundende yoyembekezera kuti mlandu wawo uzengedwe

  3. 16 August 2022

    Lyubov anaikidwa kundende ina yongoyembekezera

  4. 17 August 2022

    Lyubov anasamutsidwira kundende yoyembekezera kuti mlandu wake uzengedwe

  5. 20 September 2023

    Mlandu wawo unayamba kuzengedwa

  6. 25 December 2023

    Lyubov anatulutsidwa kundende yoyembekezera kuti mlandu uzengedwe ndipo anaikidwa pa ukaidi wosachoka panyumba

a b Pamene nkhaniyi inkalembedwa, sizinali zotheka kuti tilankhule ndi M’bale Khachaturyan komanso M’bale Yeritsyan chifukwa choti anali kundende yoyembekezera kuti mlandu wawo uzengedwe.