Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kuchokera kumazere kupita kumanja: M’bale Boris Andreyev, M’bale Anatoliy Li komanso Mlongo Nataliya Sharapova

6 MAY 2024 | INAKONZEDWANSO PA: 11 JULY 2024
RUSSIA

ZOKHUDZA ANTHU OMWE ANAGAMULIDWA KUPITA KUNDENDE | “Yehova Atithandiza Kupirira Vuto Lililonse”

ZOKHUDZA ANTHU OMWE ANAGAMULIDWA KUPITA KUNDENDE | “Yehova Atithandiza Kupirira Vuto Lililonse”

Pa 10 July 2024, Khoti la m’Boma la Khorolskiy m’chigawo cha Primorye linapeza kuti M’bale Boris Andreyev, M’bale Anatoliy Li ndiponso Mlongo Nataliya Sharapova ndi olakwa. M’bale Andreyev anagamulidwa kuti akakhale kundende kwa zaka 6, M’bale Li anamugamula zaka 6 ndi miyezi pomwe Mlongo Sharapova anamugamula zaka zitatu. Onsewa anali kale mundende yoyembekezera kuzengedwa mlandu ndipo apitiriza kukhala m’ndende.

Zokhudza M’baleyu

Mofanana ndi mmene wathandizira Anatoliy, Boris ndiponso Nataliya, sitikukayikira kuti nafenso Yehova apitiriza kuyankha mapemphero athu pa nthawi imene takumana ndi mavuto ndipo azitipatsa mphamvu kuti tipirire.​—Salimo 20:1.

Nthawi Komanso Zimene Zinachitika

  1. 28 July 2022

    Anawatsegulira mlandu

  2. 6 October 2022

    Nyumba 12 zinafufuzidwa m’mudzi wa Yaroslavsky. Boris ndi Nataliya anaikidwa m’ndende ina yongoyembekezera

  3. 7 October 2022

    Boris ndi Nataliya anasamutsidwira kundende yoyembekezera kuzengedwa mlandu

  4. 12 October 2022

    Anatoliy anaikidwa m’ndende kwa kanthawi

  5. 1 October 2022

    Anatoliy anasamutsidwira kundende yoyembekezera kuzengedwa mlandu

  6. 5 October 2023

    Anayamba kuwazenga mlandu

a b c Pamene nkhaniyi inkakonzedwa, M’bale Andreyev, M’bale Li ndiponso Mlongo Sharapova anali ali m’ndende yoyembekezera kuzengedwa mlandu, choncho sizinali zotheka kuti timve zimene anganene.