Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Mlongo Galina Komissarova

1 MAY 2024 | INAKONZEDWANSO PA: 9 JULY 2024
RUSSIA

ZOKHUDZA MLONGO YEMWE ANAPEZEDWA NDI MLANDU | “Palibenso Moyo Wina Wabwino”

ZOKHUDZA MLONGO YEMWE ANAPEZEDWA NDI MLANDU | “Palibenso Moyo Wina Wabwino”

Pa 8 July 2024, khoti la Tsentralniy m’boma Tolyatti lomwe lili m’chigawo cha Samara, linapeza kuti Mlongo Galina Komissarova ndi wolakwa ndipo linagamula kuti kwa zaka ziwiri azitsatira malamulo ena ali kunyumba kwawo. Panopa mlongoyu sakuyenera kupita kundende.

Zokhudza Mlongoyu

Mofanana ndi Galina, ifenso timaona kuti ndi mwayi waukulu kudziwa Yehova komanso kumutumikira ndi mtima wonse chifukwa timadziwa kuti ‘ndife ake.’​—Aroma 14:8.

Nthawi Komanso Zimene Zinachitika

  1. 7 September 2023

    Anamutsegulira mlandu

  2. 8 September 2023

    Nyumba ya Galina inafufuzidwa ndipo iye anafunsidwa mafunso

  3. 19 September 2023

    Analetsedwa kupita m’madera ena

  4. 18 December 2023

    Anayamba kumuzenga mlandu