Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

MAY 3, 2018
RUSSIA

A Mboni Aluza Mlandu wa Apilo, Ndipo Akuluakulu a Boma la Russia Alanda Malo Omwe Anali Ofesi ya Nthambi

A Mboni Aluza Mlandu wa Apilo, Ndipo Akuluakulu a Boma la Russia Alanda Malo Omwe Anali Ofesi ya Nthambi

Lachinayi pa 3 May 2018, Khoti la ku Saint Petersburg, linagwirizana ndi chigamulo cha mu December 2017, ndipo linavomereza kuti boma la Russia lilande nyumba zonse zomwe zinali ofesi ya nthambi ku Solnechnoye.

Ngakhale kuti sitingaletse boma la Russia kulanda malo athuwa, a Mboni za Yehova anapereka kale dandaulo lawo ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe pa nkhani ya kulandidwa kwa maofesiwa ndipo panopa khotili likuunika za nkhaniyi. Khotili linauza boma la Russia kuti pempho limene a Mboni anaperekali ndi nkhani imene khotili likufuna kuisamalira mwansanga.

Tikupitirizabe kuyembekezera Yehova yemwe ndi Mulungu wa chilungamo kuti akonze zinthu m’nthawi yake yoyenera.—Yesaya 30:18.