MAY 7, 2018
RUSSIA
Khoti la Mumzinda wa Saint Petersburg Lakana Apilo Yopempha Boma Kuti Lisalande Maofesi a Mboni za Yehova ku Russia
Pa 3 May, 2018, Khoti la mumzinda wa Saint Petersburg linakana apilo yomwe a Mboni za Yehova anapanga yopempha boma kuti lisalande ofesi yawo ya m’dzikolo ku Solnechnoye. Panopa chigamulochi chayamba kugwira ntchito ndipo boma lingatenge maofesiwo nthawi iliyonse.
Chigamulochi chikugwirizana ndi zomwe Khoti la ku Sestroretskiy linalamula kuti pangano lomwe linasainidwa zaka 17 zapitazo lonena kuti maofesi a Mboni ku Russia ali m’manja mwa bungwe la Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania lasiya kugwira ntchito. Zomwe khotili linalamula zinachititsa kuti khoti la ku Saint Petersburg lipezerepo mwayi wonena kuti maofesiwa akhala ali m’manja mwa Likulu la Mboni za Yehova ku Russia kwa nthawi yonseyi. Zimenezi zipangitsa kuti Boma la Russia lilande maofesiwa chifukwa Khoti Lalikulu Kwambiri la m’dzikoli linatseka Likulu la Mboni za Yehova ku Russia mu April 2017. Boma la Russia linagwiritsa ntchito “maganizo” opanda chilungamo amenewa pophimba anthu m’maso kuti zioneke ngati akulanda maofesiwa mwalamulo.
A Philip Brumley omwe ndi Loya Woimira Mboni za Yehova anati: “Chigamulochi n’chosayenera ndipo n’kulakwira mfundo za chilungamo. Maofesiwa anaperekedwa kwa Mulungu ndipo ankagwiritsidwa ntchito poyendetsa za Mboni za Yehova ku Russia zomwe zimachitika mwamtendere. Boma la Russia likutibera maofesiwa ndipo tipititsa nkhaniyi ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe.”