Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JUNE 22, 2018
RUSSIA

Kucheza ndi Alongo 5: Akufotokoza Zimene Apolisi Anachita Mumzinda wa Ufa ku Russia

Kucheza ndi Alongo 5: Akufotokoza Zimene Apolisi Anachita Mumzinda wa Ufa ku Russia

M’mawa pa 10 April, 2018, ofufuza komanso gulu linalake la apolisi, ena atavala zobisa nkhope komanso atanyamula mfuti, analowa m’nyumba za a Mboni ambiri n’kuchita chipikisheni mumzinda wa Ufa, lomwe ndi likulu la Bashkortostan ku Russia. M’bale Anatoliy (Tolya) Vilitkevich anamangidwa ndipo akusungidwa ndi akuluakulu a boma poyembekezera kuzengedwa mlandu. Alongo 5 ochokera ku Ufa kuphatikizapo mkazi wa m’bale Tolya dzina lake Alyona, akufotokoza mmene zimenezi zawakhudzira.