NOVEMBER 23, 2018
RUSSIA
A Mboni Ambiri Akumangidwabe ku Russia
M’mwezi wa October 2018, apolisi anathyola n’kulowa m’nyumba zoposa 30 m’chigawo chakumadzulo kwa Russia. Pa nthawiyi, abale 6 ndi alongo awiri anamangidwa n’kulamulidwa kuti akhale m’ndende poyembekezera kuzengedwa mlandu chifukwa boma likuwaganizira kuti anachita zinthu zoopsa. Panopa pali abale ndi alongo 25 omwe anaikidwa m’ndende mopanda chilungamo ndipo 18 ali pa ukaidi wosachoka panyumba.
Pa 7 October, ku Sychyovka, M’chigawo cha Smolensk—Apolisi a m’derali komanso gulu la apolisi ena ovala zobisa nkhope anachita chipikisheni m’nyumba zokwana 4 ndipo anamanga alongo awiri. Alongowa ndi a Nataliya Sorokina azaka 43 ndi a Mariya Troshina azaka 41. Patangopita masiku awiri, Khoti la m’Boma la Leninsky linagamula kuti alongo athuwa akhale m’ndende mpaka pa 19 November, 2018, poyembekezera kuwazenga mlandu. Kenako pa 16 November, 2018, Khotili linawonjezera miyezi itatu pa nthawi yoti alongowa akhale m’ndende poyembekezera kuzengedwa mlandu ndipo akhala m’ndendemo mpaka pa 19 February, 2019.
Pa 9 October, ku Kirov, M’chigawo cha Kirov—Apolisi anathyola n’kulowa m’nyumba zosachepera 19. Pa nthawiyi, akulu a mpingo 5 anawamanga kenako anawatsekera poyembekezera kuwazenga mlandu. Abale 4, ndi nzika za dziko la Russia ndipo maina awo ndi a Maksim Khalturin, a Vladimir Korobeynikov, a Andrey Suvorkov, komanso a Evgeniy Suvorkov pomwe m’bale Andrzej Oniszczuk, ndi nzika ya dziko la Poland. Pa abale ochokera m’mayiko ena omwe anamangidwa chifukwa cha zimene amakhulupirira, m’bale Dennis Christensen wa ku Denmark ndi amene anali woyamba ndipo m’bale Oniszczuk ndi wachiwiri.
Pa 18 October, ku Dyurtyuli, Republic of Bashkortostan—Apolisi anathyola n’kulowa m’nyumba zosachepera 11, ndipo analanda ndalama, makadi a ku banki, zithunzi, makalata, makompyuta, masimukadi, komanso mafoni a m’manja. A Anton Lemeshev omwe ndi mkulu anamangidwa ndipo pambuyo pake anawagamula kuti akhale m’ndende kwa miyezi iwiri poyembekezera kuwazenga mlandu. Komabe, pa 31 October, 2018, anawatulutsa m’ndendemo ndipo panopa ali pa ukaidi wosachoka panyumba.
Ngakhale kuti abale ndi alongo athuwa akukhala mwamantha chifukwa choti apolisi akhoza kuthyola nyumba zawo ndi kuwabera zinthu zawo, iwo akupitirizabe kupempherera anzawo omwe ali m’ndende ndipo akumawapatsa zinthu zofunikira komanso kuthandiza mabanja awo. Gulu lathu la abale a padziko lonse lipitirizabe kupemphera mopembedzera m’malo mwa atumiki onse okhulupirika a Yehova ku Russia, komanso kutchula ena mwa iwo ndi mayina awo m’mapemphero mpaka pamene vutoli lidzathere.—Aefeso 6:18.