Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

7 APRIL, 2016
RUSSIA

Akuluakulu a Boma la Russia Akufuna Kutseka Likulu la Mboni za Yehova M’dzikolo

Akuluakulu a Boma la Russia Akufuna Kutseka Likulu la Mboni za Yehova M’dzikolo

ST. PETERSBURG, Russia—Kwa nthawi yoyamba, akuluakulu a boma la Russia aopseza kuti atseka maofesi a Mboni za Yehova m’dzikolo.

Pa March 2, 2016, mkulu woimira boma pa milandu ku Russia analemba kalata yoopseza, yonena kuti gulu lachipembedzo la Mboni za Yehova liyenera kuthetsedwa ngati pomatha miyezi iwiri silileka kuphwanya malamulo. Dziko la Russia limati ntchito yolalikira ya a Mboni ndi yoopsa. A Yaroslav Sivulskiy omwe amalankhula m’malo mwa a Mboni ku Russia anati: “Ngati maofesi athu angatsekedwe, zingachititsenso kuti malo ena onse omwe timawagwiritsa ntchito polambira alandidwe ndipo ntchito yathu yolalikira kuno ku Russia ingaletsedwenso.”

Likulu la Mboni za Yehova m’dziko la Russia.

Zimene dziko la Russia likufuna kuchitazi n’zodabwitsa chifukwa linavomereza koyamba gulu la Mboni za Yehova kuti ndi chipembedzo chovomerezeka mwalamulo zaka 25 zapitazo. Dzikoli linavomereza kachiwiri gululi pa 29 April, 1999. Zimene akuluakulu a bomawa akuchita poopseza kuti atseka maofesiwa ndi njira yatsopano yomwe asankha kugwiritsa ntchito kuti alimbane ndi a Mboni. Maofesiwa ali ku Solnechnoy, mtunda wa makilomita 40 kum’mwera cha kum’mawa kwa mzinda wa St. Petersburg. Chaka chatha, akuluakulu a boma analetsa kuti mabuku a Mboni komanso ma Baibulo achinenero cha Chirasha asalowe m’dzikolo. Anatsekanso webusaiti ya Mboni za Yehova ya jw.org. Padziko lonse, ndi dziko lokhali limene linatseka webusaitiyi. A Sivulskiy anati: “Dziko la Russia likugwiritsa ntchito molakwa malamulo oteteza anthu ku zinthu zoopsa pofuna kuletsa ntchito ya Mboni za Yehova. Komabe tikuyesetsa kulimbana ndi zimene akuluakulu a boma m’dzikoli akuchita. Tikufuna kuti tizilambira komanso kuphunzitsa anthu Baibulo mwaufulu monga mmene takhala tikuchitira kwa zaka 125 kuno ku Russia.”

Akuluakulu a boma ku Russia akhala akulimbana ndi a Mboni za Yehova chifukwa cha mgwirizano womwe ulipo pakati pa boma ndi Tchalitchi cha Orthodox cha m’dzikolo. Ofalitsa nkhani a m’mayiko osiyanasiyana ananenanso kuti zimenezi ndi zimene zikuchititsa kuti boma la Russia lizigwiritsa ntchito malamulo molakwa pofuna kuthetsa ntchito ya a Mboni komanso zipembedzo zina zing’onozing’ono m’dzikoli. Nyuzipepala ya The New York Times inanena kuti pali “mgwirizano wamphamvu pakati pa boma ndi Tchalitchi cha Orthodox.” Nyuzipepala ya The Associated Press inanena kuti zimene boma likuchita “polimbana ndi a Mboni za Yehova zachititsa kuti magulu amene amamenyera anthu ufulu wopembedza adandaule.” Nyuzipepala ya Reuters inanena kuti boma la Russia “limagwiritsa ntchito lamulo loteteza anthu ku zinthu zoopsa polimbana ndi Mboni za Yehova komanso magulu ena ambiri azauchifwamba.” Mu December 2015, nyuzipepala yotchedwa The Independent inanena kuti boma la Russia linakhazikitsa lamulo loteteza anthu ku zinthu zoopsa ndi cholinga chofuna “kuthana ndi zigawenga komanso ziwawa zimene anthu amene amakonda kwambiri dziko lawo amachita.” Koma n’zodabwitsa kuona mmene dziko la Russia likugwiritsira ntchito lamulo limeneli, chifukwa malinga ndi lipoti la The Huffington Post la pa 20 March, 2016, lamuloli likugwiritsidwanso ntchito “poimba milandu magulu achipembedzo a mtendere” monga a Mboni za Yehova. Pofuna kuonetsetsa kuti lamuloli likugwiritsidwa ntchito moyenera, a Mboni akukambirana ndi makhoti a m’dziko la Russia komanso Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya. Iwo akuchita zimenezi ngakhale kuti pa 25 March, 2016, nyuzipepala ya The Moscow Times inanena kuti dziko la Russia lakhazikitsa lamulo latsopano “lomwe likupatsa makhoti a m’dzikoli ufulu wokana zimene makhoti a m’mayiko ena angagamule.”

Alendo ali pa malo ofikira alendo a pa likululi.

Kulikulu la Mboni za Yehova la ku Russia ndi kumene amakonza dongosolo lonse lokhudza ntchito yophunzitsa anthu Baibulo kwaulere m’dzikolo. Ogwira ntchito ena palikululi amalankhula komanso kuthandiza a Mboni ongodzipereka amene amagwira ntchito yopereka thandizo kwa anthu amene akhudzidwa ndi ngozi zadzidzidzi. M’dziko la Russia muli anthu oposa 146,000,000 ndipo kuli a Mboni oposa 175,000.

A David A. Semonian, omwe amalankhula m’malo mwa Mboni za Yehova ku likulu lawo la padziko lonse ku New York anati: “Ndife okhumudwa kwambiri kuti dziko la Russia lawopseza kuti litseka maofesi athu m’dzikolo. A Mboni za Yehova komanso anthu ena ambiri pa dziko lonse tili ndi chidwi kuti tione mmene nkhani imeneyi iyendere.”

Lankhulani ndi:

International: David A. Semonian, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Russia: Yaroslav Sivulskiy, tel. +7 812 702 2691+1 718 560 +7 812 702