Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

APRIL 17, 2018
RUSSIA

Khoti Limvetsera Apilo ya Mboni za Yehova Yodandaula Kuti Boma la Russia Lilanda Maofesi Awo

Khoti Limvetsera Apilo ya Mboni za Yehova Yodandaula Kuti Boma la Russia Lilanda Maofesi Awo

Pa 3 May, 2018, Khoti la mumzinda wa Saint Petersburg limvetsera apilo yomwe a Mboni za Yehova anapanga yokhudza chigamulo choti boma la Russia lilande ofesi ya Mboni m’dzikolo. A Mboni akaluza mlandu wa apilowu ndiye kuti chigamulochi chiyamba kugwira ntchito komanso Boma la Russia lilandadi ofesiyi nthawi yomweyo.

Kumapeto kwa chaka cha 2017, khoti laling’ono la Sestroretskiy, linakana maumboni onse osonyeza kuti ofesi ya Mboni za Yehova ya m’dziko la Russia ndi ya bungwe la Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania (WTPA). Bungweli lili ku United States ndipo cholinga chake si kupeza phindu. Bungwe la Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania lakhala likulipira msonkho wa maofesiwa m’dziko la Russia kwa zaka 17. Komabe pa 7 December, 2017, khoti laling’onoli linanena kuti maofesi a Mboni m’dziko la Russia si a bungweli. Ngati a Mboni angaluze mlandu wa apilowu komanso ngati sangathandizidwe pambuyo potsatira njira zonse zokhudzana ndi malamulo m’dziko la Russia, a Mboniwa adzatengera mlanduwu ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe.

Mlanduwu udzayamba nthawi ya 11:30 m’mawa pa 3 May 2018, ku khoti la mumzinda wa Saint Petersburg, ul. Basseynaya 6, St. Petersburg, ku Russia.