Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

MAY 2, 2018
RUSSIA

Apolisi Ayamba Kuchitira Nkhanza a Mboni za Yehova ku Russia

Apolisi Ayamba Kuchitira Nkhanza a Mboni za Yehova ku Russia

Apolisi a m’dziko la Russia analowa mwaukali m’nyumba za a Mboni za Yehova m’mizinda yosachepera 7 ya m’dzikoli. Zikuoneka kuti gulu linalake lapadera la apolisi (OMON), linachita kukonza zoti lizichitira nkhanza a Mboni ndipo akamakachita zankhanzazi nthawi zina amavala zinthu zobisa nkhope, kunyamula mfuti, kulowa m’nyumba za a Mboni popanda chilolezo, kuwaloza ndi mfuti ndiponso amakatsekera ana ndi akuluakulu omwe kuti akawapanikize ndi mafunso.

Bambo Arkadya Akopyan ndi akazi awo a Sonya komanso zidzukulu zawo

Chaka chathachi, akuluakulu a polisi anakhazikitsa ntchito yofufuza milandu yosachepera 10 ndipo anamanga azibambo 5 a Mboni. M’modzi mwa a Mboni omwe anamangidwawo ndi a Dennis Christensen omwe akhala akuwasunga m’ndende popanda kuwazenga mlandu kuyambira pa 25 May, 2017. Bambo Arkadya Akopyan a zaka 69 omwenso ndi a Mboni, panopa akuimbidwa mlandu ku Republic of Kabardino-Balkaria m’dziko la Russia. Anthu onsewa akhoza kuweruzidwa kuti akakhale m’ndende zaka ziwiri mpaka 10 chifukwa chosonkhana pamodzi n’cholinga cholambira Mulungu.

Pa 20 April, 2017, Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia linatseka Likulu la Mboni za Yehova la m’dzikolo komanso mabungwe onse 395 oimira Mboni za Yehova m’dzikolo. Pa nthawi imene khotili linkazenga mlanduwu, boma la Russia linanena kuti ngakhale kuti litseka malo onse ovomerezeka a Mboni za Yehova, zimenezi sizikutanthauza kuti liletsa wa Mboni wina aliyense kuchita zinthu zogwirizana ndi chikhulupiriro chake. Koma zimene bomali likuchita sizikugwirizana ndi zomwe linanenazi.

Popeza kuti akuluakulu a boma la Russia anatseka mabungwe oimira Mboni za Yehova komanso kulanda katundu wawo, tsopano ayamba kuukira munthu aliyense yemwe ndi wa Mboni komanso chilichonse chimene angachite chokhudza kulambira. Panopa a Mboni oposa 175,000 omwe ali m’dziko la Russia akhoza kuimbidwa mlandu ngati atapezeka akuchita zinthu zokhudza kulambira.

Kulowa M’nyumba za a Mboni, Kuwafunsa Mafunso, Komanso Kuwatsekera

Kuyambira mu January 2018, apolisi ogwira anthu ophwanya malamulo akhala akulimbana kwambiri ndi a Mboni za Yehova.

20 April, 2018, M’dera la Shuya, Ivanovo: Apolisi ogwira anthu ophwanya malamulo anapanga chipikisheni m’nyumba 4 za a Mboni. Apolisiwo anatengera a Dmitriy Mikhailov ku polisi komwe anawatsekera kenako n’kuwatulutsa. Apolisiwo anapeza bambo Mikhailov ndi mlandu ‘wochita zinthu ndi gulu lomwe limachita zinthu zoopsa,’ zomwe n’zosemphana ndi Gawo 282.2(2) la Buku la Malamulo a Zaupandu. Panopa bambo Mikhailov saloledwa kutuluka mu mzinda wa Shuya mpaka adzachite kuuzidwa.

19 April, 2018, Vladivostok: Apolisi komanso gulu lina loona za chitetezo (Federal Security Service, FSB) analowa m’nyumba ina ndipo anagwira a Valentin Osadchuk ndi azimayi ena atatu achikulire n’kupita nawo ku polisi kuti akawafunse mafunso. Apolisiwo ananena kuti a Osadchuk apezeka ndi mlandu potengera zomwe zili mu Gawo 282.2(2) la Buku la Malamulo a Zaupandu. Mlandu womwe anawapeza nawowo ukhoza kuchititsa kuti bambowa akhale m’ndende kwa zaka ziwiri mpaka 4, koma panopa anawatsekera ngakhale kuti mlandu wawo sunazengedwe. Pa 23 April, khoti la mumzinda wa Frunzenskiy linalamula kuti bambo Osadchuk aikidwe m’ndende mpaka pa 20 June, 2018, ngakhale kuti mlandu wawo sunazengedwe. Panopa akusungidwa ku ndende ina yofufuzira milandu ku Vladivostok.

18 April, 2018, M’dera la Polyarny, Murmansk: Madzulo a tsikuli, apolisi ndiponso gulu la apolisi a OMON omwe anavala zobisa nkhope ndipo ananyamula mfuti, anapita kunyumba kwa bambo Roman Markin n’kukaphwanya chitseko kenako analowa m’nyumbamo. Apolisiwo analoza bambowo ndi mfuti n’kuwauza kuti agone pansi. Mwana wamkazi wa bambowo ataona kuti apolisiwo anyamula mfuti, nthawi yomweyo anagwa pansi n’kubisa nkhope yake ndi manja. Apolisiwo anapanga chipikisheni m’nyumbayo ndipo pamapeto pake anatengera bambo Markin ku polisi komwe anakawasunga popanda kuwazenga mlandu.

Madzulo omwewo, apolisi anachitanso chipikisheni m’nyumba 14 za a Mboni a m’deralo, ndipo analanda mafoni, matabuleti, komanso katundu wina wa anthuwo. Kenako apolisiwo anatengera a Mboniwo ku polisi kuti akawafunse mafunso. Akuluakulu a m’deralo anatsegulira mlandu bambo Markin komanso bambo Viktor Trofimov omwenso ndi a Mboni. A Mboni awiriwa anawapeza ndi mlandu ‘wotsogolera zochita za gulu lomwe limachita zinthu zoopsa,’ zomwe n’zosemphana ndi Gawo 282.2(1) la Buku la Malamulo a Zaupandu. Ngati iwo angapezeke olakwa, akhoza kukhala m’ndende kwa zaka 6 mpaka 10. Panopa a Markin ndi a Trofimov akuwasunga m’ndende ina ku Murmansk.

10 April, 2018, M’Boma la Zaton, Ufa: Kuyambira 6:30 m’mawa mpaka 7:00 m’mawa womwewo, ofufuza komanso apolisi a OMON analowa m’nyumba zambiri za a Mboni ndi kuchita chipikisheni. Pamene ankachita chipikishenicho, apolisiwo ankafunsa a Mboniwo mafunso. Wapolisi wina anauza m’modzi mwa a Mboniwo kuti: “Ukangonena kuti wasiya kukhala m’gulu la Mboni za Yehova tikusiya kuti uzipita.” Wapolisi wina anauzanso munthu wina wa Mboni kuti: “Anthu inu tikuchotsani padziko lapansili.” A Mboni onse anawatengera ku polisi kuti akawajambule mizere ya zala zawo za m’manja komanso kuti akawafunse mafunso ena.

Apolisi atalowa m’nyumba ya bambo ndi mayi Khafizov, analozetsa mfuti bambo ndi mayiwa kenako n’kuchita chipikisheni m’nyumbayo. Atamaliza kuchita chipikishenicho, m’modzi mwa apolisiwo anagwira mayi Khafizova pamkono n’kuwakankhira m’galimoto ya apolisiwo, kenako anapita nawo ku polisi kuti akawafunse mafunso. Bambo Khafizov si a Mboni za Yehova.

A Anatoliy Vilitkevich ndi akazi awo a Alyona, apa n’kuti a Anatoliy asanamangidwe

Apolisi analowa m’nyumba ya a Anatoliy Vilitkevich n’kuwamanga. Iwo anauza mkazi wa bambowo kuti saona mwamuna wawoyo “kwa nthawi yayitali.” Bambo Vilitkevich anawapeza ndi mlandu ‘wotsogolera zochita za gulu lomwe limachita zinthu zoopsa,’ zomwe n’zosemphana ndi Gawo 282.2(1) la Buku la Malamulo a Zaupandu ndipo panopa anawatsekera m’ndende mmene akhalemo mpaka pa 2 June, 2018 ngakhale kuti mlandu wawo sunazengedwe. Ngati atapezeka olakwa, akhoza kukhala m’ndende kwa zaka 10.

March 2018, Oryol: Kuonjezera pa mlandu womwe a Dennis Christensen akuzengedwa, akuluakulu a boma ayambanso kufufuza a Sergey Skrynnikov omwenso ndi a Mboni, kuti aone ngati ali ndi mlandu. Zimenezi zinachitika pambuyo pochita chipikisheni m’nyumba 7 za a Mboni mu May 2017. Panopa, a Skrynnikov sanawapeze ndi mlandu koma akuwaganizira kuti anapalamula mlandu ‘wochita zinthu ndi gulu lomwe limachita zinthu zoopsa,’ zomwe n’zosemphana ndi Gawo 282.2(2). Ngati atapezeka olakwa, adzaweruzidwa kuti akakhale m’ndende kwa zaka ziwiri kapena 4.

7 February, 2018, Belgorod: Magulu akuluakulu a apolisi ogwira anthu ophwanya malamulo analowa m’nyumba zosachepera 10 za a Mboni. Apolisiwo anakakamiza eni nyumbawo kuti agone pansi komanso ena anawakanikizira kukhoma. Iwo anachita chipikisheni m’nyumbazo ndipo analanda zipangizo zamakono, mapasipoti, zithunzi, komanso ndalama. Kenako anatengera a Mboni onse ku polisi komwe anakawafunsa mafunso ndipo kenako anawatulutsa kupatulapo a Anatoly Shalyapin ndi a Sergei Voikov. Apolisi anasunga azibambo awiriwa kwa maola 48, ndipo kenako anawatulutsa. Komabe, azibambowa anauzidwa kuti sakuyenera kutuluka mu mzinda wa Belgorod.

23 January, 2018, Kemerovo: Apolisi analowa komanso kuchita chipikisheni m’nyumba 12 za a Mboni ndipo analanda zipangizo zonse zamakono, mabuku a Mboni, ndi zinthu zina zambiri zofunika. Apolisiwo asanachite zimenezi, munthu wina wamwamuna yemwe ankanamizira kuti ndi wa Mboni, ankapita kumisonkhano ya a Mboni n’kumajambula mobisa nkhani zomwe zinkakambidwa ndipo kenako anakapereka zimene anajambulazo kwa apolisi. Pogwiritsa ntchito zimene munthuyo anajambula, apolisi anayamba ntchito yofufuza mlandu.

Boma la Russia Likhoza Kulanda Ana a Mboni kwa Makolo Awo

Kuonjezera pa nkhanza zimene apolisi komanso gulu lina loona za chitetezo (FSB) akuchitira a Mboni, akuluakulu a boma la Russia alamula kuti boma likhoza kulanda ana a Mboni za Yehova kwa makolo awo kuti awaphunzitsenso zinthu zina zomwe n’zosiyana ndi zimene anaphunzitsidwa ndi makolo awo. M’chigamulo cha nambala 44 chomwe Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia linapanga pa 14 November, 2017, ananena kuti “khoti likhoza kulanda makolo ufulu wolera ana awo” ngati makolowo amachita limodzi ndi anawo zinthu za m’chipembedzo chomwe chinaletsedwa chifukwa chochita zinthu “zoopsa.”

Pa 23 November, 2017, a Unduna wa Zamaphunziro ndi Sayansi anatumiza uthenga m’dziko lonse kuuza anthu kuti ana omwe amaphunzitsidwa za m’chipembedzo chomwe ndi choopsa, ayenera kuphunzitsidwanso zinthu zina zomwe n’zosiyana ndi zomwe akhala akuphunzitsidwa ku chipembedzocho. Undunawu unangonena za magulu awiri okha a ana, omwe ndi a gulu la zigawenga lotchedwa ISIS komanso ana a Mboni za Yehova. Panopa palibe ana a Mboni omwe alandidwa kwa makolo awo.

Kodi Boma la Russia Lisiya Liti Kuchitira Nkhanza a Mboni?

Pa mayiko onse amene ndi mamembala a Bungwe la Mayiko a ku Europe, dziko la Russia lokha ndi limene likulimbana ndi gulu la Mboni za Yehova lomwe ndi lamtendere. Panopa a Mboni za Yehova ku Russia sangathenso kusonkhana poyera kuti alambire, kuwerenga ndiponso kuphunzira Baibulo. Choncho kuti asamangidwe kapena kuimbidwa milandu, ayenera kulambira mobisa ngati mmene ankachitira m’nthawi ya ulamuliro wa Soviet.

A Mboni za Yehova padziko lonse ndi okhudzidwa kwambiri ndi nkhanza zimene boma likuchitira abale awo ku Russia. Iwo akudziwa kuti zimenezi zipangitsa kuti abale awowa avutike m’maganizo, mwauzimu komanso mwakuthupi. A Philip Brumley, omwe ndi loya wa Mboni za Yehova anati: “Boma la Russia lisiye nkhanza zimene likuchitazi komanso litsatire zomwe linapangana ndi mayiko ena kuti lizilemekeza ufulu wachibadwidwe ndiponso ufulu wachipembedzo. Popeza kuti panopa akuluakulu a Bomawa asiya kulimbana ndi mabungwe oimira Mboni za Yehova n’kuyamba kumanga anthu a Mboni, kodi achitanso zotani kwa a Mboni za Yehova ku Russia?”