Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JULY 13, 2018
RUSSIA

A Mboni Oyamba Kumangidwa Monga Banja Anatsekeredwa M’ndende ku Russia

A Mboni Oyamba Kumangidwa Monga Banja Anatsekeredwa M’ndende ku Russia

Akuluakulu a boma mumzinda wa Omsk ku Russia, analamula kuti a Sergey Polyakov ndi akazi awo a Anastasia akhale m’ndende mpaka pa 6 July, 2018 poyembekezera kuwazenga mlandu. Aka ndi koyamba kuti m’modzi mwa alongo athu atsekeredwe m’ndende kuchokera pamene Khoti Lalikulu Kwambiri linaletsa ntchito za a Mboni za Yehova ku Russia.

Polankhulapo za kumangidwa kwa anthuwa, bungwe lina lofufuza komanso kufalitsa nkhani mumzinda wa Moscow (SOVA) linati: “Tikukhulupirira kuti chigamulochi komanso kuzunzidwa kwa a Mboni za Yehova, n’zosemphana ndi malamulo ndipo tikuona kuti limeneli ndi tsankho chifukwa chosiyana zipembedzo.”

Panopa ku Russia kuli abale 21 ndi mlongo m’modzi amene ali m’ndende chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Tipitirizabe kuwapempherera kuti akhale olimba mtima podziwa kuti Yehova ndi Mthandizi wawo wamkulu.—Aheberi 13:6.