Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

FEBRUARY 16, 2018
RUSSIA

Khoti la ku Oryol Liyamba Kuzenga Mlandu wa a Dennis Christensen Posachedwapa

Khoti la ku Oryol Liyamba Kuzenga Mlandu wa a Dennis Christensen Posachedwapa

Mlandu wa a Dennis Christensen udzayamba pa 19 February, 2018. A Christensen, omwe ndi nzika ya ku Denmark komanso ndi a Mboni za Yehova, akhala akuwasunga m’ndende ya mumzinda wa Oryol ku Russia kuyambira pamene anamangidwa mu May 2017.

Pa 31 January, 2018, wachiwiri kwa woimira boma pa milandu ku Oryol analemba chikalata cha masamba 76 chofotokoza kuti a Christensen ali ndi mlandu. Woimira boma pamilanduyo ananena kuti a Christensen anawapeza ndi mlandu wotsogolera ntchito ya gulu lachipembedzo lomwe khoti linanena kuti limachita zinthu zoopsa, zomwe n’zosemphana ndi Gawo 282.2(1) la Buku la Malamulo a Zaupandu m’dziko la Russia. Munthu akhoza kugamulidwa kuti akhale m’ndende zaka 10 chifukwa cha mlandu umenewu.

A Christensen sanapalamule mlanduwu. Iwo anamangidwa pa nthawi imene ankachita msonkhano wachipembedzo chawo mwamtendere limodzi ndi mkazi wawo komanso Akhristu anzawo. Mlandu wawo udzayamba pa 19 February, 2018 nthawi ya 2:30 masana pa khoti la m’chigawo cha Zheleznodorozhniy ku Oryol.