Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

NOVEMBER 29, 2018
RUSSIA

A Dennis Christensen Akulimbikitsidwa ndi Anthu a M’mayiko Osiyanasiyana

A Dennis Christensen Akulimbikitsidwa ndi Anthu a M’mayiko Osiyanasiyana

M’bale Dennis Christensen wakhala m’ndende kwa masiku oposa 525 chifukwa chochita zimene amakhulupirira ndipo wakhala akuonekera m’khoti maulendo pafupifupi 50. Khoti la m’boma la Zheleznodorozhniy ku Oryol m’dziko la Russia, ndi lomwe likuzenga mlandu wa a Christensen ndipo lakonza zoti lidzamvetsere mlanduwu cham’katikati mwa mwezi wa December. Ngakhale kuti a Christensen akhala akusungidwa m’ndende kwa miyezi yoposa 18, iwo akusangalalabe komanso ali ndi chikhulupiriro kuti zinthu ziyenda bwino. Umenewu ndi umboni woti Yehova akuthandiza a Christensen ndipo akuyankha mapemphero a abale mamiliyoni ambiri padziko lonse.

A Christensen analandira makadi komanso zithunzi kuchokera kwa a Mboni anzawo a ku Russia komanso a m’mayiko ena zosonyeza kuti amawakonda kwambiri. Pamene a khoti ankamvetsera mlandu wawo pa 30 October, a Christensen anaonetsa anthu makadi komanso zithunzi zomwe ana anawatumizira kudzera pagalasi la m’ndende yomwe ali, kuti onse amene anabwera kudzawalimbikitsa athe kuziona.

Tsiku limene khoti linkamvetsera mlandu wawo pa 30 October, 2018, pa nthawi yopuma a Dennis Christensen akuonetsa anthu kudzera pagalasi la m’ndende yawo ena mwa makalata olimbikitsa omwe analandira.

Kuwonjezera pa abale padziko lonse omwe akutsatira mlandu wa a Christensen mwachidwi, palinso anthu a m’mayiko osiyanasiyana omwe ali ndi chidwi ndi mlanduwu. Pa 21 July, 2017, bungwe lina loona za ufulu wa anthu ku Moscow (Memorial Human Rights Centre) linanena kuti a Christensen ali m’gulu la anthu omwe anamangidwa pazifukwa za ndale. Pa 20 June, 2018, komiti yoona za ufulu wa anthu ku Russia inapempha ofesi ya mkulu woimira boma pamilandu kuti itsimikize ngati kumanga a Mboni za Yehova chifukwa cha zimene amakhulupirira n’kogwirizana ndi malamulo. Pa 26 September, 2018, komiti ya ku United States yoona za ufulu wa zipembedzo m’mayiko ena, inanena kuti a Christensen ali m’gulu la “anthu omwe anamangidwa chifukwa cha zomwe amakhulupirira kuchipembedzo chawo.”

Boma la Russia linanena m’khoti kuti kutsekedwa kwa mabungwe a Mboni za Yehova sikukhudza ufulu womwe wa Mboni aliyense ali nawo wochita zimene amakhulupirira. Koma apolisi komanso akuluakulu ena a boma sakutsatira zimenezi ndipo anagwiritsa ntchito malamulo molakwika pomanga a Christensen komanso a Mboni ena ambiri, ponena kuti anawapeza ndi mlandu wochita zinthu “zoopsa.” Chaka chino, apolisi a boma la Russia anathyola n’kulowa m’nyumba za a Mboni ambiri m’madera osiyanasiyana m’dzikolo. Panopa abale ndi alongo 25 ali m’ndende, ena 18 ali paukaidi wosachoka panyumba, komanso ena oposa 40 alibe ufulu wochita zinthu zina. Zimene khoti ligamule pa mlandu wa a Christensen zithandiza kudziwa zomwe zichitikire a Mboni za Yehova oposa 90 omwe ali m’madera pafupifupi 30 ku Russia, amene akuyembekezera zotsatira za kafukufuku wokhudza milandu yawo.

Tikudziwa kuti banja lathu lapadziko lonse lipitiriza kupemphera kuti Yehova apitirize kulimbikitsa komanso kupereka mphamvu kwa abale ndi alongo amene akuimbidwa milandu chifukwa cha chikhulupiriro chawo, pamene tikuyembekezera mwachidwi tsiku limene Yehova ‘adzaonetsetsa kuti chilungamo’ chachitika kwa abale athuwa.—Luka 18:7.