Pitani ku nkhani yake

JULY 1, 2014
RUSSIA

Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya Ladzudzulanso Boma la Russia Chifukwa Chophwanyira Anthu Ufulu Wachipembedzo

Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya Ladzudzulanso Boma la Russia Chifukwa Chophwanyira Anthu Ufulu Wachipembedzo

Pa June 26, 2014, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linapereka chigamulo mokomera a Mboni za Yehova. Khotili linati a Mboni ali ndi ufulu wolambira popanda kusokonezedwa ndi akuluakulu a boma la Russia. Pa chigamulochi, chomwe oweruza onse anagwirizana, khotili linapeza kuti boma la Russia linaphwanyira anthu a Mboniwa ufulu wochita zimene akufuna komanso ufulu wotetezedwa umene umapezeka pagawo 5 ndi ufulu wonena maganizo ako, ufulu wotsatira zimene umakhulupirira ndiponso ufulu wopembedza umene umapezeka pagawo 9 la Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Ulaya. Maufuluwa anaphwanyidwa pa April 12, 2006, pamene apolisi anasokoneza msonkhano wa a Mboni komanso kugwira anthu mosemphana ndi malamulo.

Usiku wa tsikuli, a Mboni za Yehova padziko lonse anasonkhana kuti achite mwambo wawo wapachaka wokumbukira imfa ya Yesu Khristu. Mipingo iwiri ya mumzinda wa Moscow inapanga lendi holo ya sukulu ina kuti achitire mwambowu ndipo ankayembekezera kuti pafika anthu oposa 400. Mwambowu uli mkati, anangoona magalimoto 10 komanso maminibasi awiri a apolisi atulukira ndipo gulu lina la apolisi linatenga mfuti. Nthawi yomweyo anaima mozungulira holoyo ndipo anasokoneza mwambowo popanda chilolezo. Anauza anthu onse kuti atuluke kenako anasecha holoyo, kulanda mabuku a a Mboniwo ndipo anatenga mokakamiza azibambo 14. Anapita nawo kusiteshoni ya apolisi ya m’deralo ndipo anawatsekera. Loya woimira a Mboni amene anatsekeredwawo atauzidwa anathamangira kusiteshoniyo kuti akawathandize. Atangofika, apolisi anamusecha n’kumukankhira pansi. Kenako anamuika mpeni pakhosi n’kumuopseza kuti akasumira mlandu apolisiwo, anthu a m’banja lake aona zakuda. Patadutsa maola oposa atatu, anthu amene anatsekeredwawo anatulutsidwa n’kuwauza kuti azipita kwawo.

Nikolay Krupko, amene anatsogolera pa mlanduwu

Bambo Nikolay Krupko, limodzi ndi a Mboni ena atatu amene anatsekeredwa aja anasumira apolisiwo chifukwa chosokoneza msonkhano wachipembedzo komanso kuwatsekera mosemphana ndi malamulo. Anthuwa anatumiza dandaulo lawo ku khoti la ku Lyublino komanso la mumzinda wa Moscow koma makhoti onsewa anakana dandauloli. Kenako mu June 2007, anthuwa anatumiza dandaulo lawo ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya.

Pa June 26, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya, linagamula kuti: “Khoti laona kuti, ngakhale zitakhala kuti akuluakulu a boma sanadziwitsidwe za msonkhano, koma ngati ochita msonkhanowo sanasokoneze mtendere wa anthu, apolisi alibe mphamvu zosokoneza msonkhano umene ukuchitika mwamtendere ndipo zimenezi ‘n’zosaloleka m’dziko lomwe aliyense ali ndi ufulu.’ . . . Zimenezi zikugwiranso ntchito pa mlanduwu womwe anthu omwe ankapanga msonkhano umene ukunenedwawu sankapanga phokoso kapena kusokoneza mtendere wa anthu ena chifukwa mwambowu unkachitikira mu holo. Zimene apolisi anachitazi, posokoneza mwambowu ali ndi mfuti komanso kuchita zachiwawa ali ambirimbiri ndiponso kugwira anthuwa n’kuwatsekera kwa maola atatu, n’zosayenera chifukwa anasowetsa mtendere anthu osalakwa. Izi zili choncho ngakhale kuti akuluakulu a boma anaona kuti mwambowu ndi wosaloleka chifukwa chakuti sanawadziwitse.”

Aka ndi kachitatu kuti khotili lipeze boma la Russia ndi mlandu wophwanya ufulu wa a Mboni za Yehova. Mu 2007, pa mlandu wakuti a Kuznetsov and Others v. Russia, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linagamula kuti dziko la Russia linaphwanya Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Ulaya pamene akuluakulu a boma anasokoneza msonkhano wa a Mboni ovutika kumva ku Chelyabinsk. Mu 2010, pa mlandu wakuti Jehovah’s Witnesses of Moscow v. Russia, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linagamula kuti boma la Russia linalakwa chifukwa apolisi a mumzinda wa Moscow anathetsa gulu lovomerezeka la Mboni za Yehova la mumzindawu mosemphana ndi malamulo. Mu 2013, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linapereka chigamulo pa mlandu wakuti Avilkina and Others v. Russia. Khotili linati akuluakulu a boma la Russia anaphwanjira anthu ufulu wosungiridwa chinsinsi pamene akuluakulu oimira boma pa milandu a ku St. Petersburg anakakamiza anthu kuti aulule zinthu zachinsinsi zokhudza matenda awo.

Zigamulo za Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulayazi zikupereka umboni winanso wosonyeza kuti akuluakulu a boma la Russia akamaletsa a Mboni za Yehova kulambira, amakhala akuchita zosemphana ndi Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Ulaya lomwe dzikoli linavomereza kuti lizitsatira.