Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

OCTOBER 1, 2014
RUSSIA

A Mboni za Yehova a ku Samara Apanga Apilo Mlandu Wokhudza Kutsekedwa kwa Bungwe Lawo Lovomerezeka ndi Boma Kukhoti Lalikulu Kwambiri la ku Russia

A Mboni za Yehova a ku Samara Apanga Apilo Mlandu Wokhudza Kutsekedwa kwa Bungwe Lawo Lovomerezeka ndi Boma Kukhoti Lalikulu Kwambiri la ku Russia

Pa October 8, 2014, Khoti Lalikulu Kwambiri la Ku Russia liweruza mlandu umene a Mboni za Yehova a ku Samara apanga apilo. Mlanduwu ndi wokhudza kutsekedwa kwa bungwe lawo lovomerezeka ndi boma. Khoti laling’ono la m’derali linagamula kuti bungweli limachita zinthu monyanyira komanso zosokoneza maganizo a anthu. Khoti Lalikulu likapanda kusintha chigamulochi, ndiye kuti a Mboni oposa 1,500 a ku Samara akhala pamavuto aakulu.

Ofesi ya ku Samara Yoimira Boma pa Milandu Inagwiritsa Ntchito Njira Zachinyengo

Mlandu wokhudza bungwe la Mboni za Yehova lovomerezeka ndi boma ku Samara unayamba mu April 2014, pamene ofesi yoimira boma pa milandu m’derali inasuma kukhoti kuti bungweli litsekedwe chifukwa “chochita zinthu monyanyira komanso zosokoneza maganizo a anthu.” Khoti la m’derali lisanaweruze mlanduwu, ofesi yoimira bomayi inaletsa bungweli kuti lisamagwire ntchito zake komanso analanda nyumba imene bungweli linkagwiritsa ntchito. Mlanduwu usanakambidwe nkomwe, unduna woona zachilungamo m’dzikoli unaika bungwe la Mboni za Yehova lovomerezeka ndi bomali m’gulu la zipembedzo zomwe zatsekedwa chifukwa chochita zinthu monyanyira komanso zosokoneza maganizo a anthu. Kenako, pa May 29, 2014, woweruza milandu wa kukhotili dzina lake Shabayeva anagamula mlanduwu mokomera ofesi yoimira boma pa milandu. Iye analamula kuti bungwe la Mbonili litsekedwe komanso kuti nyumba imene bungweli linkagwiritsa ntchito ilandidwe.

Aka si koyamba kuti ofesi ya ku Samara yoimira boma pa milandu isumire bungweli n’cholinga choti litsekedwe. Mu 2009, ofesiyi inakasuma kukhoti koma kenako inanena kuti mlanduwu usapitirire. Pa mlandu waposachedwawu, akuluakulu a boma anagwiritsa ntchito njira ina pofuna kukwaniritsa cholinga chawo.

Makhoti a ku Russia Atseka Bungwe la Mboni ku Samara pa Zifukwa Zosamveka

Mu January 2013 ndi mu January 2014, apolisi a m’derali anasecha nyumba zimene a Mboni anapanga lenti kuti azigwiritsa ntchito polambira ndipo akuti anapezamo mabuku a chipembedzo omwe anali m’gulu la zinthu zosokoneza maganizo a anthu zomwe ndi zoletsedwa m’dziko lonse la Russia. Ofesi yoimira boma pa milandu ya mumzinda wa Samara inachenjeza bungwe la Mboni ku Samara, zokhudza mabuku amene apolisi a m’derali anapeza mu 2013. Apolisiwa atapezanso mabuku ena mu January 2014, ofesi yoimira boma inasumira bungweli. Pa March 7, 2014, khoti la Sovetskiy lomwe lili ku Samara linapeza kuti bungweli ndi lolakwa ndipo linagamula kuti bungweli lilipire chindapusa cha ndalama zokwana madola 1,383, a ku America. A Mboni a ku Samara akukhulupirira kuti apolisiwa ndi amene anaika mabuku pa nthawi zonse zimene anafufuzazo. A Mboniwa sakugwirizana ndi chigamulo chimene khotili linapereka chakuti mabuku awo ndi osokoneza anthu ndipo apanga apilo ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya.

Ofesi yoimira boma pa milandu ya mumzinda wa Samara itapititsa nkhaniyi ku khoti laling’ono la ku Sovetskiy, khotili linagamula kuti bungwe la Mboni ndi lolakwa. Kenako mu April 2014 ofesiyi inasumira bungweli mlandu wochita zinthu zosokoneza maganizo a anthu ku khoti lalikulu la mumzinda wa Samara. Anachita izi pofuna kutseka bungweli. Loya wa Mboni za Yehova anayesetsa kukambirana ndi a Shabayeva amene ankaweruza mlanduwu kuti panalibe zifukwa zomveka zotsekera bungweli. Ananenanso kuti pa zinthu zimene a Mboni za Yehova komanso bungwe lawoli limachita kapena kukhulupirira, palibe zimene zimasokoneza maganizo a anthu. Anaonjezeranso kuti apolisi ndi amene anaika mabuku amene akuti ali m’gulu la zinthu zosokoneza maganizo a anthu zomwe ndi zoletsedwa m’dziko la Russia. Komabe izi sizinamveke, ndipo woweruza mlanduyo anatseka bungwe la Mboni m’dera la Samara.

Kodi Boma la Russia Lipitiriza Kuphwanyira Anthu Ufulu Wolambira?

Zimene zinachitika poweruza mlandu wa ku Samara, zikufanana ndi zimene akuluakulu a ku Russia anachita poweruza mlandu wa Mboni za Yehova ku Taganrog. Akuluakuluwa anagwiritsa ntchito molakwika lamulo la dziko la Russia loteteza anthu ku zinthu zosokoneza maganizo pofuna kuthetsa bungwe loimira Mboni za Yehova. Mu 2009 anakwanitsadi kuthetsa bungwe loimira Mboni za Yehova ku Taganrog ndipo kenako anatsegulira mlandu wa Mboni aliyense. Milanduyi inapangitsa kuti a Mboni za Yehova okwana 7 azunzidwe komanso kutsekeredwa m’ndende chifukwa chingopezeka pa misonkhano ya chipembedzo chawo basi. Zimenezi zikhoza kuchitikiranso a Mboni za Yehova a ku Samara.

Kodi Boma la Russia lidzasiya liti kusokoneza ufulu wolambira wa a Mboni za Yehova? Kuyambira mu June 2014, a Mboni a m’madera osiyanasiyana m’dzikoli, akhala akuimbidwa milandu yabodza chifukwa chopezeka akugawa mabuku a chipembedzo chawo, omwe bomali limati ndi osokoneza maganizo a anthu. Komabe a Mboni za Yehova a ku Samara akukhulupirira kuti Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia liweruza mlandu wawo mwachilungamo.