18 JULY, 2017
RUSSIA
Khoti Lalikulu Kwambiri M’dziko la Russia Silinasinthe Chigamulo Chimene Linapereka Choletsa Ntchito ya Mboni za Yehova
Pa 17 July, 2017 Khoti Lalikulu Kwambiri M’dziko la Russia linagamula kuti silisintha chigamulo chimene linapereka poyamba choletsa ntchito ya Mboni za Yehova m’dzikolo. Zimene boma la Russia lachitazi ndi kuphwanya malamulo a padziko lonse omwe amapereka ufulu wopembedza kwa munthu aliyense. Panopa ndiye kuti a Mboni za Yehova sakuloledwanso kupembedza m’dziko lonse la Russia.
Oweruza akuluakulu atatu a khotili anakana apilo imene a Mboni za Yehova anachita ndipo ananena kuti akugwirizana ndi zimene a Yuriy Ivanenko anagamula pa 20 April, 2017. A Yuriy anagamula mogwirizana ndi zimene a Unduna wa Zachilungamo m’dzikolo ananena kuti, “likulu la Mboni za Yehova ku Russia litsekedwe komanso kuti boma lilande zinthu zonse zimene likululi limayang’anira.”
Zimene khotili lagamula zikuika pangozi moyo wa a Mboni za Yehova oposa 175,000 omwe ali m’dzikolo. A Philip Brumley omwe ndi loya wa Mboni za Yehova anati: “A Mboni za Yehova padziko lonse akudera nkhawa kwambiri abale ndi alongo awo a ku Russia. Zimene khoti la apilo lagamula zichititsa kuti a Mboni za Yehova azichitiridwabe nkhanza zosiyanasiyana komanso kuimbidwa milandu yongowanamizira. Tsopano a Mboni za Yehova ayamba kuonedwa ngati anthu osafunika m’dziko lawo lomwe.”
A Mboni za Yehova apanga apilo za nkhaniyi ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya komanso ku Komiti ya United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu. Panopa a Mboni za Yehova padziko lonse akupitirizabe kupemphera kuti boma la Russia lisinthe maganizo ake pa chigamulochi komanso kuti liyambe kulemekeza ufulu wa anthu. Zimenezi zithandiza kuti a Mboni za Yehova ‘akhale ndi moyo wabata ndi wamtendere, ndiponso kuti akhale odzipereka kwa Mulungu mokwanira,’ mogwirizana ndi zimene zili palemba la 1 Timoteyo 2:2.