Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

DECEMBER 11, 2017
RUSSIA

Zimene Khoti la Russia Lagamula Zipereka Mpata Woti Maofesi a Mboni Alandidwe

Zimene Khoti la Russia Lagamula Zipereka Mpata Woti Maofesi a Mboni Alandidwe

Pa 7 December 2017 khoti la m’dera la Sestroretskiy, linapereka chigamulo chake mokomera loya wa boma ndipo linanena kuti pangano lomwe lakhalapo kwa nthawi yayitali, pakati pa boma ndi Likulu la Mboni za Yehova latha. Ngati khoti silisintha chigamulochi, ndiye kuti akuluakulu a boma agwiritsa ntchito chigamulochi molakwika pofuna kukwaniritsa cholinga chawo cholanda maofesi a Mboni ku Solnechnoye kufupi ndi St. Petersburg.

Zaka 17 zapitazo, maofesi a Mboni ku Russia anasainiridwa kuti ali m’manja mwa bungwe la ku United States la Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania. Anachita zimenezi posainirana pangano ku boma ndipo nawonso akuluakulu a boma ku Russia anagwirizana nazo moti anauzidwanso za kutalika kwa nthawi imene panganolo litenge. Bungwe la Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania linapereka mphamvu ku Likulu la Mboni ku Russia kuti liziyang’anira ntchito za a Mboni za Yehova m’dzikolo ndipo linkapereka misonkho yonse ku boma.

Potengera zimene Khoti Lalikulu Kwambiri linagamula pa 20 April 2017, zoti mabungwe a Mboni atsekedwe, ntchito zawo ziletsedwe komanso kuti zinthu zawo zilandidwe, loya wa boma analengeza kuti pangano la zaka 17 lija linatha. Zimenezi ndi zoona chifukwa nthawi yake inathadi zaka zingapo zapitazo. Mlanduwu unatenga maola 4 ndipo a Mboni anapereka maumboni awo omveka bwino osonyeza kuti boma linavomereza pangano lawo ndipo khoti likuyenera kuganizirapo bwino. Koma pambuyo pake woweruza wina dzina lake Bogdanova anagamula mlanduwu mokomera loya wa boma.

A Mboni za Yehova ali ndi masiku 30 oti achitire apilo nkhaniyi.