Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

DECEMBER 27, 2018
RUSSIA

Khoti ku Russia Lagamula Kuti a Arkadya Akopyan a Zaka 70 Ndi Olakwa

Khoti ku Russia Lagamula Kuti a Arkadya Akopyan a Zaka 70 Ndi Olakwa

Lachinayi pa 27 December, woweruza milandu wina dzina lake Oleg Golovashko wa khoti la m’boma la Prohladniy ku Russia, analengeza chigamulo chomwe khotili linapanga pa mlandu wa M’bale Arkadya Akopyan. Khotili linagamula kuti M’bale Akopyan, yemwe ali ndi zaka 70 ndipo anapuma pa ntchito yake ya utelala, agwire ntchito yothandiza dera lake kwa maola 120 pomuganizira kuti anatuma anthu ena omwe si a Mboni kuti akagawire mabuku a zinthu zoopsa. Zimene m’baleyu akumuganizirazi n’zoseketsa.

Ngakhale kuti M’bale Akopyan sanalamulidwe kuti akhale m’ndende, chigamulochi chikuphwanya kwambiri ufulu wawo. Choncho akachita apilo za nkhaniyi ku khoti lina lalikulu.

Posachedwapa, tikuyembekezera chigamulo cha khoti pa mlandu wa a Dennis Christensen. Tikupemphera kuti Yehova apitirize kuthandiza komanso kutonthoza abale ndi alongo athu amene akumangidwa ku Russia chifukwa cha chikhulupiriro chawo.—2 Atesalonika 2:16, 17.