Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

DECEMBER 11, 2017
RUSSIA

Khoti la ku Russia Limvetsera Apilo pa Mlandu Wakuti Baibulo Lili m’Gulu la “Zinthu Zoopsa”

Khoti la ku Russia Limvetsera Apilo pa Mlandu Wakuti Baibulo Lili m’Gulu la “Zinthu Zoopsa”

Pa 6 December 2017, Khoti la Mumzinda wa Leningrad linamvetsera mlandu womwe a Mboni anachita apilo pa chigamulo chomwe khoti lina laling’ono linapereka choletsa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika la m’Chirasha.

Khoti la Mumzinda wa Leningrad linayamba kumvetsera mlanduwu pamene maloya oimira a Mboni anatsutsa chigamulo chomwe khoti la mumzinda wa Vyborg linapereka potengera zomwe ochita kafukufuku anapeza ngati umboni wa mlandu wa a Mboni. Khoti la Vyborg silinapeze chilichonse mu Baibulo la Dziko Latsopano chosonyeza kuti Baibuloli lili “m’gulu la zinthu zoopsa” ngati mmene ochita kafukufukuwo ankanenera. Komabe khotili linagwiritsa ntchito mawu omaliza a ochita kafukufukuwo, onena kuti Baibulo la Dziko Latsopano ndi loopsa chifukwa choti olemba Baibuloli anagwiritsa ntchito dzina la Mulungu, lakuti Yehova. Maloya a Mboniwo anauza khoti kuti asaiwale kuti kuchokera kalekale nzika za ku Russia zakhala zikugwiritsa ntchito dzina la Mulunguli ndipo limapezekanso m’Mabaibulo ambiri a ku Russia. Maloyawa anapezeraponso mwayi wotsutsa zimene ochita kafukufukuwo ananena zoti Baibulo la Dziko Latsopano si Baibulo chifukwa palibe paliponse pamene panalembedwa kuti ndi Baibulo. Potsutsa mfundo imeneyi, maloyawo anagwiritsa ntchito mawu oyamba a m’Baibulo la mu 2007. Mawuwo ananena kuti: “Baibulo latsopano lokonzedwanso m’Chirasha.”

Khoti la Mumzinda wa Leningrad litamva zimenezi linaitanitsa anthu omwe anakachita kafukufuku aja kuti awafunsenso bwinobwino. Pa nthawiyi khotili linaimitsa kaye mlanduwu kuti udzakambidwenso pa 20 December 2017 nthawi ya 2:30 masana.