Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

MAY 1, 2018
RUSSIA

Khoti Limvetsera Apilo Yopempha Kuti Ofesi ya Nthambi Yakale Isalandidwe ku Russia

Khoti Limvetsera Apilo Yopempha Kuti Ofesi ya Nthambi Yakale Isalandidwe ku Russia

Lachinayi pa 3 May, 2018 nthawi ya 11:30 m’mawa, khoti la mu mzinda wa Saint Petersburg lidzamvetsera apilo yomwe a Mboni anapanga. Iwo anapanga apiloyo chifukwa cha chigamulo chomwe chinaperekedwa mu December 2017 chimene chingachititse kuti a boma alande nyumba za ofesi ya nthambi yakale ku Russia. Ngati apiloyi ingakanidwe, ndiye kuti nthawi yomweyo boma lilanda malo omwe panamangidwa nyumba zokwana 14.