Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

DECEMBER 20, 2018
RUSSIA

Mlandu wa M’bale Arkadya Akopyan Adzawumvetsera Komaliza pa 21 December

Mlandu wa M’bale Arkadya Akopyan Adzawumvetsera Komaliza pa 21 December

M’bale Arkadya Akopyan yemwe ali ndi zaka 70, akaonekera m’khoti komaliza pa 21 December, 2018. A Akopyan kwawo ndi ku Kabardino-Balkaria m’dziko la Russia ndipo anapuma pa ntchito yawo ya utelala. Kwa chaka choposa chimodzi, akhala akuzengedwa mlandu ku khoti la m’boma la Prohladniy, ndipo akhala akudziteteza pa zomwe akuwaganizira zoti anagawira anthu ena mabuku “oopsa” komanso ‘kuyambitsa chidani pa nkhani zachipembedzo’ pa nthawi yomwe ankakamba nkhani ya m’Baibulo ku Nyumba ya Ufumu.

Mu May 2018, woweruza milandu analamula kuti bungwe lina la ku Russia lomwe lili ndi akatswiri ofufuza za milandu (Russian Federal Center of Judicial Expert Studies) lione nkhani yojambulidwa yomwe M’bale Akopyan anakamba. Pa 4 December, 2018, khoti linalengeza kuti ofufuzawa anapeza kuti M’bale Akopyan ananena zinthu zopangitsa anthu omwe ankamumvetsera kuti azidana ndi anthu azipembedzo zina. Sizikudziwika ngati woweruza milandu adzalengeze chigamulo chokhudza nkhaniyi pa 21 December. Komabe, ngati M’bale Akopyan angapezeke wolakwa, akhoza kulipitsidwa chindapusa chachikulu kapena kutsekeredwa m’ndende kwa zaka 4.

M’bale Akopyan ndi mmodzi mwa a Mboni za Yehova oposa 100 omwe akuzengedwa milandu chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Choncho, tikupempherera abale ndi alongo omwe akuyesetsa kukhala okhulupirika kuti apitirize kukhala ndi mtendere womwe Mulungu yekha ndi amene amapereka.—Aefeso 6:11-14, 23.