DECEMBER 30, 2012
RUSSIA
“Sitili M’chaka cha 1937”
Pa April 16, 2012, munthu wina wa Mboni za Yehova dzina lake Aleksandr Solovyov, analamulidwa kulipira ndalama zokwana madola 30 a ku America chifukwa chokonza msonkhano wa chipembedzochi. Msonkhanowu unachitikira mu holo ina imene anachita kupanga lendi. Izi zinachitika mumzinda wa Perm womwe uli m’chigawo chapakati cha dziko la Russia.
Woweruza milandu wa kubwalo lalikulu atamvetseranso mlanduwu komanso kumva maumboni onse, anagamula kuti a Solovyov asalipire ndalama zimene khoti laling’ono la mumzindawo linawalamula.
Wowerezayu atawerenga chigamulochi, anayang’ana munthu wa Mboni yemwe ankaimbidwa mlanduyo n’kunena kuti: “Ngakhale kuti palibe lamulo lokhazikika pa nkhaniyi komanso kuti anthu ena anaiweruza mwatsankho, sitili m’chaka cha 1937 pamene tinkangoweruza anthu kuti ndi olakwa popanda kumva mbali zonse komanso kufufuza maumboni. Ndikanakonda anthu a mumzinda uno akanamayamikira ntchito yabwino yophunzitsa anthu makhalidwe abwino imene anthu inu mukugwira.
”
Mu July chaka cha 1937, Stalin anakhazikitsa Gawo 00447 la malamulo ndipo zimenezi zinazunzitsa anthu ambiri. Munthu aliyense amene ankakhala ndi maganizo osiyana ndi zimene boma linkafuna ankamangidwa komanso kumutengera kukhoti n’kukamuimba mlandu popanda umboni weniweni. Maumboni amasonyeza kuti anthu masauzande ambiri anatumizidwa kundende ndipo anthu ena opitirira 300,000 anaphedwa.