Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

NOVEMBER 24, 2017
RUSSIA

Khoti la ku Oryol Lawonjezeranso Nthawi Yoti a Dennis Christensen Akhale M’ndende

Khoti la ku Oryol Lawonjezeranso Nthawi Yoti a Dennis Christensen Akhale M’ndende

ZOMWE ZANGOCHITIKA KUMENE: Pa 22 December 2017, Khoti la Sovietsky linakana apilo yomwe loya wa a Christensen anapereka yopempha kuti a Christensen awamasule kaye poyembekezera mlandu wawo. Nthawi yoti a Christensen akhale m’ndende podikira mlandu wawo itha pa 23 February 2018. Kenako akaonekeranso ku khoti kachiwiri kuti akayankhe mlandu wophwanya malamulo.

Pa 20 November 2017, khoti la Sovietsky la mumzinda wa Oryol linamvetsera mlandu wa a Christensen womwe unatenga maola atatu. Pamapeto pa mlanduwu m’pamene khotili linawonjezera nthawi yoti a Christensen akhale m’ndende kwa miyezi ina itatu mpaka pa 23 February 2018. Aka si koyamba kuti khotili liwonjezere nthawi yoti a Christensen akhale m’ndende. Iwowa anamangidwa mu May 2017 atawapeza pamsonkhano wachipembedzo ku Oryol. Pa nthawiyo apolisi anasokoneza misonkhano ya chipembedzo imene inkachitika mwamtendere.

A Christensen ndi a Mboni za Yehova ndipo ndi nzika ya ku Denmark. Asanamangidwe, Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia linaletsa ntchito za chipembedzo cha Mboni za Yehova ponena kuti ndi zobweretsa chisokonezo. Pa nthawiyi khotili linawonjezeranso nthawi yoti a Christensen akhale m’ndende ndi cholinga chopereka mpata kwa ofufuza kuti asonkhanitse maumboni onse otsimikizira kuti misonkhano ya Mboni za Yehova ndi yosemphana ndi malamulo. Podikira kufufuzidwa kwa nkhaniyi, a Christensen anapempha kuti akakhale kaye pa ndende ya panyumba koma khotili linakana. Khotili linakananso zomwe boma la Denmark linanena zowatsimikizira kuti podikira mlanduwu, lingathe kusunga a Christensen m’dziko lawo. Boma la Denmark linalonjeza kuti silidzawabwezera pasipoti yawo kapena kuwathawitsa m’dzikolo.

Mkazi wa a Christensen ndi nzika ya ku Russia. Pamene a Christensen ankamangidwa, iwo ndi akazi awo anasonkhana ndi anzawo pamsonkhano wa chipembedzo pogwiritsa ntchito ufulu wawo mogwirizana ndi malamulo. Khotili likhoza kulamula kuti asungidwebe m’ndende kwa zaka ziwiri poyembekezera kuzengedwa kwa mlandu wawo. Ndipo ngati atadzawapeza kuti ndi olakwa, akhoza kudzawagamula kuti akhale m’ndende kwa zaka kuyambira 6 mpaka 10.