Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

A Mboni za Yehova akuimba nyimbo kumisonkhano ku Rostov-on-Don, Russia

SEPTEMBER 22, 2016
RUSSIA

GAWO 1

Zimene Akatswiri Ena Ananena: Dziko la Russia Likugwiritsa Ntchito Molakwika Lamulo Loteteza Anthu ku Zinthu Zoopsa Pofuna Kuletsa Ntchito ya Mboni za Yehova

Zimene Akatswiri Ena Ananena: Dziko la Russia Likugwiritsa Ntchito Molakwika Lamulo Loteteza Anthu ku Zinthu Zoopsa Pofuna Kuletsa Ntchito ya Mboni za Yehova

Nkhaniyi ndi yoyamba pa nkhani zitatu zomwe zikufotokoza zimene ananena akatswiri a zachipembedzo, a zandale, zachikhalidwe cha anthu komanso a maphunziro a ulamuliro wa Soviet Union.

ST. PETERSBURG, Russia—Ofesi ya loya Wamkulu Woimira Boma pa Milandu m’dziko la Russia ikuyesetsa kuti a Mboni za Yehova aikidwe m’gulu la anthu ochita zinthu monyanyira komanso zosemphana ndi malamulo. Ngati khoti litagamula mokomera mkulu woimira bomayu ndiye kuti ofesi ya Mboni za Yehova idzatsekedwa komanso ntchito ya Mboni za Yehova idzaletsedwa m’dzikolo. A Mboni anapanga apilo pa nkhaniyi ndipo khotilo linapitiriza kuzenga mlanduwu pa 23 September, 2016.

Dziko la Russia likuimba mlandu a Mboniwo pogwiritsa ntchito molakwika malamulo oteteza anthu ku zinthu zoopsa. Akatswiri a maphunziro akunena kuti limeneli ndi “tsankho” ndipo ndi “zolakwika kwambiri” komanso “zosamveka.”

Dr. Derek H. Davis

A Derek H. Davis, omwe anali mkulu wa nthambi ina ya maphunziro okhudza zachipembedzo ndi za m’dziko pa yunivesite ya Baylor ananena kuti: “Boma likuyenera kumalimbana ndi zinthu zoopsa zomwe zingawonongedi moyo wa anthu. Kulimbana ndi zinthu zina zosiyana ndi zimenezi kungakhalenso kuchita zinthu zoopsa.”

Dr. Mark Juergensmeyer

A Dr. Mark Juergensmeyer, omwe ndi mkulu wa bungwe lina pa yunivesite ya California, ku Santa Barbara, anafotokoza chifukwa chake boma la Russia likulimbana ndi a Mboni omwe sachita zachiwawa. Iwo anati: “Kuphwanyira anthu ufulu wolambira ponamizira kuti akufuna kulimbana ndi gulu lochita zoopsa ndi kulakwa kwambiri.” Mogwirizana ndi mfundo imeneyi a Dr. Jim Beckford, omwe ndi membala wa British Academy anafotokoza kuti: “Anthu ena a Tchalitchi cha Orthodox ku Russia anapanga mgwirizano ndi akuluakulu a boma pofuna kulimbikitsa zofuna zawo komanso kulimbana ndi anthu amene akuwaganizira kuti akupikisana nawo.”

Dr. Jim Beckford

Akatswiriwa anafotokozanso kuti vuto si kugwiritsa ntchito molakwika lamulo kokhako ayi koma vuto linanso ndi lakuti lamuloli palokha limapereka mpata woti ena azichitira za nkhanza anzawo. Bungwe loona za Ufulu wachibadwidwe ku Moscow linanena kuti: “Monga mmene takhala tikunenera lamulo loteteza anthu ku zinthu zoopsa, ndi lovuta kumvetsa tanthauzo lake ndipo ndi losamveka bwinobwino, choncho lakhala ngati chida chabwino chozunzira andale komanso magulu ena omwe amawaona kuti ndi osavomerezeka.”

Dr. Emily B. Baran

Wachiwiri kwa mphunzitsi wina wa mbiri yakale pa yunivesite ya Middle Tennessee State ku Russia, dzina lake Dr. Emily B. Baran, ananena kuti: “Anthu a m’dziko la Russia akuyenera kuda nkhawa ndi zomwe boma likupanga polimbana ndi a Mboni chifukwa zimenezi zikusonyeza kuti boma ndi lokonzeka kuphwanya ufulu wa magulu ena komanso timagulu tina ting’onoting’ono.”

Lankhulani ndi:

Kuchokera Kumayiko Ena: David A. Semonian, Office of Public Information, 1-718-560-5000

Russia: Yaroslav Sivulskiy, 7-812-702-2691