Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

MAY 23, 2018
RUSSIA

Mayiko Ena Adzudzula Boma la Russia Pozunza a Mboni za Yehova

Mayiko Ena Adzudzula Boma la Russia Pozunza a Mboni za Yehova

Bungwe la European Union komanso dziko la United States linalemba zikalata posonyeza kudandaula ndi zimene boma la Russia lachita pozunza a Mboni za Yehova. Zikalatazi zikusonyeza kuti zimene boma la Russia linanena n’zabodza. Bomali linanena kuti ngakhale kuti litseka malo ovomerezeka a Mboni za Yehova, zimenezi sizikhudza ufulu womwe wa Mboni wina aliyense ali nawo wochita zinthu zogwirizana ndi chikhulupiriro chake. Komabe, mogwirizana ndi zimene bungwe la European Union linalemba, “zimene bomali linanena sizikugwirizana ndi zimene [boma la Russia] likuchita.” Poyerekezera zimene boma la Russia linanena ndi zimene bomali likuchitira a Mboni, dziko la United States m’chikalata chake, linanena kuti “zimene likuchitazi n’zosiyana ndi zimene linanena.”

Akuluakulu a boma la Russia anaika m’ndende azibambo 8 omwe ndi a Mboni ndiponso panopa akufufuza milandu 12 m’mizinda 11. Ngakhale kuti tikudandaula kwambiri ndi chiwerengero chomwe chikuwonjezereka cha katundu yemwe akulandidwa, tikudera nkhawa kwambiri za Akhristu omwe akuzunzidwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo.

Bungwe la European Union komanso dziko la United States apempha boma la Russia kuti lilemekeze malamulo ake popereka “ufulu wonena maganizo ako, ufulu wotsatira zimene umakhulupirira ndiponso ufulu wopembedza kapena wokhulupirira.”

Zikalatazi muzipeza apa:

https://www.osce.org/permanent-council/381820

https://www.osce.org/permanent-council/381823