10 APRIL, 2015
RUSSIA
Wa Mboni Wina wa ku Russia Anatola Ndalama Zokwana Mayuro 6,000 Ndipo Anazibweza kwa Mwini Wake
ST. PETERSBURG, Russia—Mu November 2014, mayi Svetlana Nemchinova, omwe ndi a Mboni za Yehova, anatola envelopu mumsewu wina, ndipo ataitsegula anapezamo ndalama za mayuro zokwana 6,000, zomwe ndi zofanana ndi madola 6,800 a ku United States. Kenako anayamba kufufuza mwini wake wa ndalamazo ndipo patapita nthawi anamupeza n’kumubwezera ndalama zakezo. Nkhaniyi inaulutsidwa pa TV komanso pa wailesi ndipo inalembedwanso m’nyuzipepala zingapo za pa intaneti.
A Nemchinova amagwira ntchito yosesa mumsewu mumzinda wa Vologda, womwe uli pamtunda wa makilomita 450 kumpoto chakum’mawa kwa mzinda wa Moscow. Ndiye tsiku lina akugwira ntchito anaona envelopu yopanda dzina. Ataitsegula anapeza kuti mkati mwake munali ndalama zambiri. Umenewutu unali mwayi wawo chifukwa mayiwa limodzi ndi ana awo atatu, amakhala m’kanyumba kakang’ono ndipo ndi osauka. Mayiwa anati: “Nditatola ndalamazo, sindinakhale ndi maganizo akuti laponda la mphawi. Ndinkadziwa kuti mwini wake wa ndalamazo akudandaula kwambiri.”
Mayiyu anayesetsa kuti apeze amene anataya ndalamazo moti anamata mapepala odziwitsa anthu kuti ngati pali wina amene wataya ndalama, amupeze. Anamata mapepalawa panyumba zina zomwe zinali pafupi ndi malowo. Koma ataona kuti palibe amene wabwera, mayiwo anatenga ndalamazo n’kupita nazo kubanki ina. Anapita nazo kubankiyi chifukwa mkati mwa envelopu ija munali kapepala kosonyeza kuti munthu amene anataya ndalamazo anazitenga kubankiyo. Ogwira ntchito kubankiko ananena kuti mwini wa ndalamazo anali a Pavel Smirnov. Kenako anayamba kuwafufuza ndipo atawapeza anawauza kuti ndalama zawo zapezeka. Anawauzanso kuti anatola ndalamazo ndi mayi Nemchinova.
Nyuzipepala ina ya ku Russia inati: “Mayiwa ndi ochititsa chidwi kwambiri chifukwa iwowo akuona kuti zimene achitazi n’zimene amayenera kuchita basi. Akuoneka kuti amakonda Mulungu kwambiri ndipo akuti amawerenga Baibulo tsiku lililonse.” Mayi Nemchinova anafotokozera nyuzipepalayi kuti achita zimenezo chifukwa chotsatira mfundo ya m’Baibulo yomwe imapezeka pa Mateyu 7:12 yomwe imati: “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zomwezo.”
A Smirnov, omwe ndi mwini wa ndalamazo, ndi katswiri wa zojambulajambula ndipo ali ndi luso kwambiri, moti anatulukira kasakanizidwe kenakake ka penti. Bambowa anafotokoza kuti ankasungira ndalamazo kuti akagule chipangizo chosakanizira penti choti adzagwiritse ntchito pochita kafukufuku. Bambowa anati: “Sindikudziwa kuti ndiwathokoze bwanji mayiwa. Zimene achitazi zikusonyeza kuti anthu abwino adakalipo padzikoli. Ngati anthu oti tikhoza kuwakhulupirira akupezekabe, sitingalakwe titanena kuti ‘kunja kuno Mulungu alipodi.’”
Yankhulani ndi:
Kuchokera ku Mayiko Ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000
Russia: Yaroslav Sivulskiy, tel. +7 812 702 2691