Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

MAY 1, 2018
RUSSIA

Akuluakulu a Boma ku Russia Akufuna Kulanda Malo ndi Nyumba za Bungwe la Mboni za Yehova la ku America

Akuluakulu a Boma ku Russia Akufuna Kulanda Malo ndi Nyumba za Bungwe la Mboni za Yehova la ku America

NEW YORK—Lachinayi pa 3 May, 2018, khoti la mumzinda wa Saint Petersburg lidzamvetsera apilo yomwe a Mboni za Yehova anapanga pambuyo pa chigamulo choti boma lilande ofesi yawo yakale ku Russia. Ngati apilo imeneyi ingakanidwe, boma likhoza kulanda malo pamene pali nyumba zokwana 14. Malowa ndi aakulu maekala 25 ndipo ndi a ndalama pafupifupi madola 31.8 miliyoni a ku America.

Pachigamulo choyamba chomwe chinaperekedwa ndi khoti la m’boma la Sestroretskiy mu December 2017, khotilo linanyalanyaza umboni woti ofesi ya Mboni za Yehovayo ndi ya bungwe la ku United States la Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, lomwe cholinga chake si kupanga phindu. Malowa anakhala a Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania mu 2000, ndipo pofika pano bungweli lalipira ndalama za msonkho za malowa ku boma la Russia zokwana madola 3 miliyoni a ku America. Ngakhale kuti boma la Russia likudziwa kuti a Mboni anatsatira malamulo pamene ankapanga zoti malowa akhale m’manja mwa bungwe la Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania zaka 17 zapitazo, khoti la ku Sestroretskiy linanena kuti pangano loti malowa ali m’manja mwa wa bungwe la Watch Tower latha ntchito. Kenako khotilo linanena kuti mwini wake wa malowo ndi bungwe la Mboni za Yehova la m’dzikolo (Administrative Center). Chifukwa choti bungwe la Mbonili linathetsedwa ndi Khoti Lalikulu Kwambiri mu 2017, ngati a Mboni angaluze mlandu wa apilowu, ndiye kuti boma lidzalanda malowo nthawi yomweyo.

Mlandu wa apilowu udzayamba kuzengedwa 11:30 m’mawa ku khoti la mu mzinda wa Saint Petersburg, ul. Basseynaya, 6, St. Petersburg, Russia.

Lankhulani ndi:

Ku Mayiko Ena: David A. Semonian, Ofesi Yoona Zofalitsa Nkhani, +1-845-524-3000