Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

RUSSIA

Mfundo Zachidule Zokhudza a Mboni ku Russia

Mfundo Zachidule Zokhudza a Mboni ku Russia

Poyamba a Mboni za Yehova ankapembedza mwamtendere ku Russia pa nthawi imene analembetsa monga chipembedzo chovomerezeka ndi boma mu 1992. Ndiyeno mu 1999, a Mboni analembetsanso chipembedzo chawo ku boma mogwirizana ndi lamulo lokhudza ufulu wopembedza (Law on Freedom of Conscience and Religious Associations). Pali mabungwe oimira a Mboni za Yehova mahandiredi ambiri omwe analembetsedwa ndipo akugwira ntchito zawo m’dziko lonselo.

Komabe, a Mboni za Yehova amakumana ndi mavuto ambiri omwe amaika ufulu wawo wopembedza pa chiopsezo. Kuyambira mu 2009, akuluakulu a boma akhala akuthandiza pa ntchito yolimbana ndi a Mboni m’dziko lonselo pogwiritsa ntchito molakwika Lamulo Lolimbana ndi Zinthu Zoopsa. Makhoti a ku Russia ananena kuti mabuku ambiri a Mboni, kuphatikizapo webusaiti yovomerezeka ya a Mboni, ya jw.org, ndi zoopsa. Apolisi akhala akuchita chipikisheni m’nyumba za a Mboni mahandiredi ambiri komanso malo awo olambirira. Oimira boma pamilandu akhala akusumira a Mboni milandu yosiyanasiyana chifukwa chopezeka pa misonkhano yachipembedzo chawo kapena kuchititsa misonkhanoyo.

Ngakhale kuti Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe komanso mabungwe a m’mayiko ena akhala akudzudzula boma la Russia, akuluakulu a boma la Russia achita zochepa kwambiri kuti athetse nkhanza komanso tsankho limene a Mboni za Yehova akukumana nalo. Akuluakulu a boma omwe amaonetsetsa kuti anthu akutsatira malamulo akhala akuchita khama kwambiri pofuna kuletsa ntchito za a Mboni za Yehova.