Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

27 JULY, 2017
RUSSIA

Boma la Russia Likufuna kuti Khoti Ligamule kuti Baibulo ndi Buku Lolimbikitsa Uchigawenga

Boma la Russia Likufuna kuti Khoti Ligamule kuti Baibulo ndi Buku Lolimbikitsa Uchigawenga

NKHANI MWACHIDULE: Khoti la mumzinda wa Vyborg lalamula kuti lidzapitiriza kumva mlandu pa 9 August, 2017.

Pa 28 July, 2017, Khoti la mumzinda wa Vyborg lidzapitiriza kumva mlandu womwe cholinga chake n’chofuna kudzagamula kuti Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lomwe limafalitsidwa ndi a Mboni za Yehova m’Chirasha, ndi lolimbikitsa za uchigawenga. Mlanduwu anauimitsa kaye mu April 2016, woweruza atagwirizana ndi maganizo a maloya a boma ofuna kukhazikitsa komiti yapadera yoti ifufuze umboni wotsimikizira kuti Baibulo la Dziko Latsopano limalimbikitsa za uchigawenga.

Patapita nthawi, anamaliza kafukufukuyo ndipo zotsatira zake anazipereka kukhotili pa 22 June, 2017. Ochita kafukufukuyu anapereka umboni woti Baibuloli ndi loyambitsa chisokonezo ndipo a Mboni za Yehova sanadabwe nazo chifukwa ankadziwa kale kuti anthuwo anali ndi maganizo amenewo. Mulipoti lawo, ofufuzawo ananena kuti Baibulo la Dziko Latsopano “si Baibulo.” Iwo anafotokoza izi pofuna kupewa Lamulo limene limaletsa anthu kunena kuti mabuku opatulika monga Baibulo, ndi olimbikitsa uchigawenga. Kuwonjezera pamenepo, ochita kafukufukuyu anafotokoza mmene Baibuloli linamasuliridwira kuti ukhale ngati umboni wa maganizo awo. Mwachitsanzo, ananena kuti m’Baibulo la Dziko Latsopano anamasulira zilembo zinayi zoimira dzina la Mulungu a kuti “Yehova.” Iwo ananena kuti a Mboni anamasulira chonchi zilembozi kuti zigwirizane ndi zikhulupiriro zawo.

a Zilembo zinayi zoimira dzina la Mulungu m’Chiheberi (יהוה), zinamasuliridwa kuti YHWH kapena JHVH ndipo zimapezeka m’malo pafupifupi 7,000 m’Malemba Achiheberi.