Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

AUGUST 22, 2018
RUSSIA

Anali M’ndende Koma Pano Ali pa Ukaidi Wosachoka Panyumba

Anali M’ndende Koma Pano Ali pa Ukaidi Wosachoka Panyumba

Abale awiri omwe posachedwapa analamulidwa kuti akhale pa ukaidi wosachoka panyumba ali ndi maloya awo. Kuchokera kumanzere kupita kumanja: loya Vitaly Svintsov, Vladimir Kochnev, Aleksandr Suvorov, ndi loya Egiazar Chernikov.

Pa 3 August, 2018, woweruza milandu wina dzina lake Inna Yangubayeva wa Khoti la mzinda wa Leninsky ku Orenburg, m’dziko la Russia, analamula kuti M’bale Vladimir Kochnev ndi M’bale Aleksandr Suvorov akhale pa ukaidi wosachoka panyumba pambuyo potsekeredwa m’ndende kwa masiku 78. Pa tsiku lomwelinso, khoti la m’dera la Magadan linalamula kuti M’bale Konstantin Petrov akhale pa ukaidi wosachoka panyumba pambuyo potsekeredwa m’ndende kwa masiku 64. Tikusangalala kuti abale athu atatuwa salinso m’ndende pano, komabe milandu yawoyi ikudikira chigamulo cha khoti ndipo ngati angapezeke olakwa, atha kulamulidwa kuti akakhale kundende mpaka zaka 10.

Pofika pa 16 August, a Mboni okwana 9 aikidwa pa ukaidi wosachoka panyumba pomwe 25 ali m’ndende zosiyanasiyana m’dziko la Russia. Abale ndi alongo enanso okwana 30 anauzidwa kuti asaine chikalata chosonyeza kuti sadzatuluka m’dera lomwe akukhala popanda kutenga chilolezo kwa apolisi. Tikupitiriza kupempherera abale ndi alongo athu omwe akukumana ndi zokhomazi m’dziko la Russia.—2 Akorinto 1:11.